A Chimwendo ayendera shopu yomwe idapsa ndi moto mu msika wa Zomba

Advertisement
Richard Chimwendo Banda in Zomba

Nduna yamaboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda ayamikira akulu akulu a Khonsolo ya mzinda wa Zomba chifukwa chothimitsa mwachangu moto womwe udabuka Loweruka mu shop ya a James Kanjinga mu msika waukulu wa Zomba.

A Chimwendo Banda adayamikira izi mu msika waukulu wa Zomba pomwe adayendera shopu ya hadiweya ya a Kanjinga yomwe idapsa ndi moto ndipo katundu adapseratu.

Iwo ati Boma lilindi chisoni chachikulu chafukwa cha ngoziyo ndipo adati awonetsetsa kuti buzinesi yawo ibwelerenso ngati momwe idalili poyamba.

A Chimwendo Banda adayamikira khonsolo ya mzinda wa Zomba chifukwa chofika mwachangu kudzathimitsa motowo ndipo adati idzi zidapangitsa kuti motowo usafalikire ma shopu ena amu msikawo.

Ndunayi idapempha akulu akulu omwe amayang’anira msikawu kuti ayankhule ndi ochita malonda mu msika wa Zomba kuti adzipewa kuchita zinthu zomwe zingapangitse kubukitsa moto wolutsa.

“Ndife okhudzidwa kwambiri ndikupsa kwa shopu ya a James Kanjinga chifukwa adali kuchita bizinesi yomwe imatukula banja lawo komanso achibale. Tidziwe kuti Boma silingalembe ntchito anthu onse nchifukwa chake limalimbikitsa kuchita malonda,” adatero a Richard Chimwendo Banda.

Poyankhulapo, a James Kanjinga adathokodza Ndunayi chifukwa chobwera kudzawatonthoza panthawi yomwe shop yawo yapsa ndi moto.

Iwo adaphempha boma kuti liwathandidze ndi ngongole kuti athe kuyambiranso kuchita bizinesi popeza katundu wao yense adapseratu.

Pauledowu a Chimwendo Banda adalo ndi wachiwiri kwa mlembi wankulu wachipani cha Malawi Congress Party (MCP) ndi akulu akulu ena ndipo adapepesa ndi ndalama yokwana 500 thousand kwacha.

Advertisement