Mzuni yatsekedwa kutsatira zionetsero za dzulo

Advertisement
Mzuzu University

Kutsatira zionetsero zomwe ophunzira aku Mzuzu University anachita dzulo lachisanu, akuluakulu a sukuluyi alamula ophunzira onse kuti achoke pasukuluyi mam’mawa wa lero loweruka.

Malingana ndi kalata yomwe akuluakulu a sukuluyi atulutsa, ophunzira sakuloledwa kupezeka pa sukuluyi padakali pano.

Ophunzirawa anachita zionetsero dzulo lachisanu ati pofuna kuti sukulu fees itsike.

Mwazina iwo anayatsa moto komanso kutchinga nsewu wa M1 wapakati pa Karonga komanso Mzuzu zomwe zinakakamiza apolisi kuwathira utsi okhetsa msonzi ndi cholinga choti abalalike.

Akuluakulu a sukuluyi ati apanga chisankho chotseka kaye sukuluyi ndi cholinga chofuna kuteteza katundu ndipo ophunzira adziwitsidwa mtsogolomu za tsiku lomwe sukuluyi itsekulidwenso ndizoyenera kuchita pomwe akubwerera pa malopa.

Malingana ndi malipoti, a face to face amalipira K650,000 ndipo a ODL K600,000 pomwe amene akupitiriza maphunziro awo akumalipira K800,000 enanso K1 million.

Advertisement