Ndimadyera momwemo: Mr Jokes akana kugulilidwa mano

Advertisement
Mr Jokes a Malawian comedian

…wapempha kuti angomupatsa ndalamazo

Katswiri pa nthabwala m’dziko muno Andrea Thonyiwa yemwe amadziwika kwambiri ndi dzina loti ‘Mr Jokes’, wakanitsitsa mwayi omwe anthu ena anamupatsa kuti apite m’dziko la South Africa kuti akamugulire mano.

Malipoti pa masamba a mchezo akusonyeza kuti gulu la a Malawi ena omwe ali m’dziko la South Africa linachita nsonkhensonkhe kuti Mr Jokes apite m’dzikolo akawagulire mano osakhala achilengedwe.

Zikuveka kuti anthuwa anasonkherana ndalama ya mayendedwe, malo ogona, zakudya, ndalama yogulira mano komaso ndalama yolira akatswiri achipatala omwe amayembekezeka kugwira ntchito yoyikilira manoyo.

Koma poti ukayipa umadziwa nyimbo, Mr Jokes atutumutsa gulu kamba koti amenyetsa nkhwangwa pamwala kuti sangachite chibwana chanchombo lende ngati chimenecho.

Malingana ndi kilipi (audio clip) yomwe Mr Jokes anayankha anthuwa pa maganizo awo kudzera pa WhatsApp, wati kuti iye ayikidwe mano atsopano nde kuti malonda ake ochita zisudzo atha kukhala opanda chikoka.

Iwo ati ngakhale kuti mano ochita kuyikilirawo amawafuna, koma akuona kuti anthu amene amakonda nthabwala zawo atha kusiya kuzikonda ngati iwo angayikitse manowo, choncho ati nkwabwino akhale ndi magweruwo.

“Choyamba ndithokoze chifukwa cha mtima wanu wabwino pondiganizira kuti Mr Jokes abwere ku South Africa mudzamuikitse mano. Ndinkhani yabwino kwambiri ndipo ndiyosangalatsa komaso anthu abwino ngati inu ndinu osowa kwambiri.

“Komano mukuona bwanji sindiye kuti mukandiyikitsa mano nde kuti pamenepo mwandiphela bizinezi, mukuona bwanji? Buzinezi ithela pompo chifukwa choti ineyo ndimadyera mommo. Inde ndichilema choti munthu sunganene kuti chimandisangalatsa, komano anthu anakhala ngati azolowera m’mene ndimaonekera nde apeze kuti Mr Jokes aja ali ndi mano, basitu mbola amwene hahahaha, imeneyo nde ndiyosagwira,” anatero Mr Jokes mu kilipiyo.

Iwo apeleka maganizo oti gululo lingowapatsa ndalama zomwe anasonkhelana kuti awagulire manozo ndicholinga choti apangire zinthu zina zomwe zithaso kuwapindulira pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

“Bwanji tipange chonchi: mukuona bwanji mutagondipatsa ndalamayo kuti indithandize mu zinthu zina? Sindikudziwa maganizo anu koma ineyo ndimaona ngati chanzeru nchongondipatsa ndalamayo.

“Panopa manowo sakufunika, ikufunika kwambiri ndi ndalamayo, ndikadzawafuna mwina mtsogolomu ndidzakuuzani koma pano ikufunika ndi ndalamayo. Nde bwanji mungonditumizira ndalamayo ndiwone nayo zochita chifukwa kungoyikitsa manowo nde kuti anthu ambiri asiyaso kundikonda,” anaonjezera choncho Thonyiwa.

Kuwonjezera apo, Mr Jokes pothilira ndemanga za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la fesibuku ati: “Zinthu zina zikamabwela zimaoneka ngati m’dalitso koma zikufuna zikugwetse. Nanga m’malo mondipatsa ndalamayo tidzikaikananso mano? Manowo ine andipindulira chani?”

Anthu ena omwe ayikira ndemanga za nkhaniyi pa tsamba la mchezo la fesibuku, agwirizana ndi maganizo a katswiri wochita nthabwalayo.

“Ndipo live, Mano mkachaniso anga umanva kuyabwa usinini,” watelo munthu wina pa fesibuku poyikira mlomo za nkhaniyi.

Pakadali pano sizikudziwika kuti gulu la asamaliya achifundowa lichita chiyani potsatira yankho lomwe Mr Jokes awapatsa pa maganizo awo.

Advertisement