Shingo “Haye haye” siwamisala – watsutsa Rick Pack yemwe amamuyang’anira

Advertisement
Rabson Juma

Makono ano masamba a mchezo akugwira ntchito yotamandika yofalitsa ma uthenga osiyanasiyana ngakhale kuti ena sawagwiritsa bwino ntchito. Pa matsamba amchezowa ena amawatenga ngati njira imodzi yochotsera nkhawa poti anthu ena amayika makanema osangalatsa ndinso oseketsa.

M’modzi mwa anthu omwe watchuka kusangalatsa anthu mumasambawa ndi Rabson Juma yemwe amadziwika bwino ndi dzina lokuti “Shingo” kapenanso kuti “Haye haye” ngakhale kuti anthu ena amati ndiwamisala koma yemwe amamuyang’anira Haleem Kasimu, dzina lodyera Rick Pack watsutsa zankhaniyi.

“Tikati wamisala nde kuti okudya zotoleza komanso sangagwire ganyu pomwe a Shingo kukacha amadziwa zochita ngakhale kuti anabadwa kuti pena m’mutu siziyenda koma kunena kuti ndi wamisala ndikulakwitsa,” anatero Rick Pack,yemwe amakhala ku Mangochi limodzi ndi Shingo.

Anapitilira kunena kuti,” Shingo ndiwachikulire kwa ine, kwambiri wakula ndi azimalume anga, takhala naye nthawi yayitali moyandikana moti pano anasanduka m’bale moti ine mothandizana ndi abale anga timamuthandiza mu zinthu zambiri.”

Anthu ambiri pa masamba a mchezo akhala akumunena Rick kuti amamudyera Shingo ndalama zomwe amapanga pa tsamba la Facebook komanso kuti bwenzi atapita naye ku Chipatala pozindikira kuti makanema a Haye Haye amayankha zosemphana akamafunsidwa.

“Chiyambireni sindinalindireko ndalama ku Facebook ngati m’mene ena amaganizira komanso Shingo zakusayenda kwake kwa mutu ndi vuto lachibadwidwe zoti ku chipatala sizingatheke,” iye anatero.

Koma anatsindika kuti pakadali pano anthu ena akumapempha kuti awapangire promo zinthu zawo ndipo ndalama imeneyi imamuthandizara zinthu zina ndi zina zomwe zimafunika pa moyo wake watsiku ndi tsiku.

“Zinthu ngati zingapitilire kuchita bwino kutsogoloko ndi khumbo langa kuti tizammangire nyumba kumudzi kwawo kwa Katema m’boma lomwelo la Mangochi,” anaonjezera motero.

M’buyomu pa masamba a mchezo takhalanso tikuona mkulu wina dzina lake Gopani yemwenso amachita zinthu zofananirako ndi Shingo ndipo anagwedeza kwambiri moti mpaka ena anamupangira nyimbo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.