Mnyamata wa zaka 18 wamangidwa chifukwa chogwirilira mwana wa zaka zitatu

Advertisement

Wyson Salad wa zaka 18 amumanga ku Balaka pomuganizila kuti anagwirilira mwana wa zaka zitatu.

Mneneri wa polisi ya Balaka a Gladson M’bumpha ati izi zinachitika pa 1 September, 2023 ndipo oganizilidwayo, yemwe ndi amalume ake a mwanayo, wamangidwa dzulo.

A M’bumpha ati pa 1 September nthawi ya kumasana a Salad omwe amachita bizinesi ya kabaza anatenga mwanayu panjinga yawo kuti akamugulire masilipasi.

Nthawi yomwe agogo ake amwanayu amamusambitsa, mwanayu anaulula kuti amamva ululu ndipo atafunsidwa ananena kuti a Salad anamulowetsa chinthu ku malo obisika.

Mayiwa anatengera nkhaniyi kupolisi komwe mwanayu anatengeredwa kuchipatala chachikulu cha Balaka ndipo achipatala anatsimikiza kuti mwanayo wagwiliridwa.

Pakadali pano a Salad mchitokosi cha apolisi ndipo akuyembekezereka kukaonekera ku bwalo la mlandu ndikukayakha mlandu ogwirilira.

Iwo amachokera m’mudzi wa Mphepozinayi, mfumu yaikulu Msamala m’boma la Balaka.

Advertisement