Thupi la Khansala Kajosolo wa ku Zomba layikidwa m’manda

Advertisement

Thupi la Malemu Khansala Rams Kajosolo wa Ntiya Ward mu Mzinda wa Zomba yemwe adali wachipani cha UTM layikidwa mmanda lero kumudzi kwao ku Mdeka kwa T/A Chigalu Boma la Blantyre.

Poyankhula pamwambo woyika m’manda thupili, wofalitsa nkhani kuchipani cha UTM a Felix Njawala adati mtsogoleri wachipachi Saulosi Chilima yemwenso ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino ndiwokhumudwa kwambiri chifukwa cha ifa ya Khansala Kajosolo.

A Njawala adati ngati chipani chidzamukumbikira Khansala Kajosolo chifukwa adali olimbikira kuchipani komanso adali wokonda mtendere.

Poyankhulanso m’malo mwa makhansala amu Mzinda wa Zomba Khansala Steven Bamusi adati khonsolo ya Mzinda wa Zomba yataya munthu ofunikira kwambiri popedza adali olimbikira kunkhani yachitukuko ndipo pamene amamwalira adali wapampando wa komiti yowona zantchito mumzindawu.

Khansala Bamusi adatinso malemu Kajosolo adali wokonda mtendere pakati pa anzake ndipo anthu aku wadi kwake adapanga chitukuko chochuluka.

Mu mau ake, Phungu wamdera lapakati mu Mzinda wa Zomba Wolemekedzeka Bester Awali adati malemu Khansala Kajosolo adali munthu okonda chitukuko ndipo Mzinda wa Zomba wasintha kwambiri kumbali yachitukuko chifukwa malemuwa adali okonda chitukuko.

Poyankhulanso, Phungu wa Blantyre North a Francis Phiso adati ndiwokhumudwa kwambiri chifukwa cha imfa ya Khansala Kajosolo popeza adali mmodzi mwa anthu ofunira zabwino mdziko lake.

Malemu Khansala Rams Kajosolo adamwalira m’bandakucha watsiku lachinayi kuchipatala chachikulu cha Zomba ndipo asiya mkazi ndi ana asanu.

Ena mwa anthu odziwika bwino omwe adali nawo pamwambo operekedza thupi lamalemu Khansala Rams Kajosolo ndi monga Mfumu ya Mzinda wa Blantyre Khansala Wild Ndipo, Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Davie Maunde, Phungu wamdera lapakati mu Mzinda wa Zomba Bester Awali, Phungu wamdera lakumpoto Boma la Blantyre Francis Phiso, Sheik Dinala Chabulika, Dr James Mpunga, T/ A Chigalu komanso Senior Chief Chowe a Boma la Mangochi.

Follow us on Twitter:

Advertisement