Mulandu wa a Bushiri waimitsidwa

Advertisement
Prophet Shepherd Bushiri and his wife Mary Bushiri

Bwalo la milandu ku Lilongwe laimitsa mulandu wa a Shepherd Bushiri komanso mayi akunyumba kwawo a Mary Bushiri omwe akuyankha milandu yomwe adapalamula mdziko la South Africa.

Banja la a Bushiri likuyankha milandu yokhudza kuzembetsa ndalama ku South Africa ndipo boma la dzikolo likufuna awiriwa atumizidwe mdzikolo kuti akayankhe milanduyi.

Lero mmawa bwalo la milanduli linalephera kupitiliza kumva mulanduwu kamba koti mmodzi mwa oyimira mbali ya boma pa mulandu wa a Bushiri a Dzikondianthu Malunda adwala ndipo analephera  kufika ku bwaloli. 

Annelene van de heever, omwe ndi mmodzi mwa oyimira mbali ya a Bushiri, amayenera kupitilizabe kufunsa mafunso a Sibongile Mzinyathi omwe ndi mboni ya mdziko la South Africa.

Lachinayi, oweruza milandu Madalitso Khoswe Chimwaza anagamula mokomera mbali ya a Bushiri kuti oyimila mbali yawo apitilize kufunsa mafunso mboni imodzi ndicholinga chofuna kumvetsetsa za mulandu omwe a Bushiri akuyankha.

Mlanduwu auyimitsa mpaka pa 17 July, 2024.

Advertisement