Aphunzitsi alangiza boma kuti lichite zomwe lidalonjeza

Advertisement
students Malawi

Aphunzitsi omwe adamaliza maphunziro awo kuchokera m’sukulu zosula aphunzitsi akupulayimale zosiyanasiyanasiyana m’dziko muno m’gawo la IPTE 14, 15 ndi 17, koma sadalembedwebe ntchito ndi boma, apempha boma kuti lisamatsogoze ndale koma kukwanilitsa zomwe lidalonjeza.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe aphunzitsiwa alembera maunduna aboma ndipo mwambo opereka kalatazi wachitika dzulo pa 17 May, 2024 kulikulu laboma ku Capital Hill munzinda wa Lilongwe.

Kudzera muchikalatachi, aphunzitsiwa ati atopa ndikudikila komanso kumangomvera malonjezano osakwanilitsidwa kuchokwera ku boma

Iwo ati adindo m’maunduna a boma akuyenera kugwira ntchito yabwino yomwe anthu adzawakumbukile nayo pamene adzasiye mipando yawo ndikupereka mwayi kwa ena kuti agwireko ntchito namakondwera ndi zokoma za mipando yawo zomwe iwo pano akusangalala nazo kamba ka maudindowa.

Aphunzitsiwa apereka masiku okwanira khumi (10) ku boma komanso adindo ena owona ntchito zamaphunziro kuti apereke mayankho, ndipo ngati sachitapo kanthu pakutha kwa masiku khumi, iwo achita china chilichonse chimene angafune kuti akakamize boma kuti liwalembe ntchito.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.