Kampani yopanga magetsi ya Electricity Generation Company (EGENCO) yatsimikizira mtundu wa aMalawi kuti ayiwale zakuthimathima kwa magetsi ponena kuti magetsi achuluka ndipo akuchita kusefukira.
Izi ndi malingana ndi mkulu wa EGENCO a William Liabunya omwe loweruka lapitali amayankhula ndi imodzi mwa nyumba zowulutsira mawu mdziko muno mupologalamu yomwe amakamba nkhani yokhudza magetsi.
A Liabunya anati iwo anadabwitsika ndipo anagwetsa misozi ya chimwemwe sabata yatha pomwe analandira malipoti kuchokera kwa ogwira ntchito awo kuti makina ena opangira magetsi anathimitsidwa kaye kaamba koti magetsi anachuluka.
Iwo anati zonsezi ndi kaamba kakuyambiraso kugwira ntchito kwa makina ena kumalo opangira magetsi a Kapichira ndipo anaonjezera kuti ichi ndichitsimikizo kuti aMalawi ayiwale zogona mudima.
“Kapichira yayaka, makina awiri akuyenda, mdima tathana nawo. Dzulo (lachisanu pa 7 April) ndinali ndi chimwemwe kwambiri nditaona kuti sola itayaka ku Salima tinathimitsa makina awiri akuti low demand (anthu ogwiritsa ntchito achepa magetsi achuluka), magetsi adzadza akutayikira.
“Ine kuona lipoti akuti tathimitsa makina awiri, Tedzani, Nkula, akuti ayi magetsi akusowa kolowera. Ine ndinati Ambuye ndinu wabwino. Panopa magetsi ndiokwanira. Ndikukhulupilira kuti ngakhale ndi amzathu a ESCOM titha kuvomelezana kuti kuthimitsa magetsi tiyeni tiiwale,” anatelo a Liabunya.
Mkuluyu analimbikitsa anthu mdziko muno kuti azikhala ndi chikhulupiliro kuti mzika za dziko lino ziliso ndikuthekera kugwira bwino ntchito zina za chitukuko cha dziko lino ndipo ati anthu achotse maganizo omadalira azungu.
“Ndilimbikitse anthu kuti tiyeni tiziika chikhulupiliro pa anthu athu. Nthawi zambiri anthu timaona ngati mzunga ndiwanzeru kuposa munthu wakuda koma zitha kutheka wakuda kukhala wa nzeru kuposa mzungu. Ndithokoze apulezidenti athu kaamba koti anatikhulupilira kuti titha kuigwira ntchitoyi,” anaonjezera a Liabunya.
Nkhaniyi ikudza kutsatira kukozedwa ndi kuyambiraso kugwira ntchito kwa makina awiri kumalo opangira magetsi a Kapichira zomwe zaonjezeretsa mphavu ya magetsi ndi 64.8 megawatsi.
Kukozedwaso kwa makina awiriwa komwe akuti kwatenga ndalama zokwana K10 biliyoni, kwapangitsa kuti vuto lakuthimathima kwa magetsi mdziko muno lichepe ndipo tikunena pano madera ena akulowa sabata yachiwiri magetsiwa asanathime.
Komabe ngakhale zili choncho, kampani yogawa magetsi ya ESCOM ikumatulutsabe mndandanda wa momwe magetsi athimile mmadera ena zomwe zikutanthauza kuti anthu mmadera ena akugulabe makandulo mwakathithi.
Follow us on Twitter: