Pamene anthu akupitilira kukakamiza nduna yowona za mphamvu ya magetsi a Ibrahim Matola kuti apepese pazomwe anayankhula dzulo m’boma la Dedza, a Matola ati anthu sakutanthauzira bwino mwambi omwe iwo anapeleka.
A Matola akudzudzulidwa kaamba konena kuti anthu omwe akudandaula kuti a Lazarus Chakwera akuyendayenda kwambiri ndi achule.
Potsatira nkhaniyi, anthu oyankhula pazinthu zosiyanasiyana komaso a Malawi ena makamaka m’masamba amchezo, ati ndunayi ikuyenera ipepese kumtundu wa a Malawi kaamba kazomwe anayankhulazi.
Koma ndunayi kudzera kwa oyiyankhulira wawo Marshall Dyton, ati mwambi omwe anapeleka pamwambo okhazikitsa ntchito yopanga magetsi kuchokera ku mphavu yadzuwa, samatanthauza kuti anthu mdziko muno ndi achule.
Ndunayi yati iwo amangofuna kumulimbikitsa mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera kuti ngakhale angakumane ndizomutsitsa zochuluka, koma apitilire ndi masomphenya ake pankhani yachitukuko.
A Matola ati iwo paumunthu wawo sangafike mlingo onyoza a Malawi mpaka kuwayelekeza ndi chule pamene ndi omweso akuwagwilira ntchito.
“Ngati mutamvera zonse zomwe zinayankhulidwa, mutha kumvetsetsa kuti kodi tanthauzo lake la m’mwambiwo linali chiyani. Palibe pomwe panenedwa kuti a Malawi omwe akudandaula za mavuto a zachuma mdziko muno ndi a chule.
“Mwambi omwe unapelekedwa unali oti kulira kwa achule sikumaletsa njovu kumwa madzi kutanthauza kuti a Chakwera asabwelere mmbuyo kuchita chitukuko mdziko muno powopa zomwe otsutsa boma komaso anthu akulankhura. Sananene kuti a Malawi ndi achule, ayi,” atelo a Matola kudzera kwa owayankhulira.
Ndunayi yati ikuganiza kuti anthu sakuvetsetsa zomwe amatanthauza pa mwambiwu kaamba koti makanema omwe akugawidwa mmasamba amchezo okhudza nkhaniyi, ndiongodula, sizonse zomwe anayankhula.