Papa wa mathanyula

Advertisement

Papa Francis yemwe ndi mkulu wa mpingo wa Katolika pa dziko lapansi wati anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha ali ndi ufulu omanga banja  ndipo mpingo wa Katolika ukuyenera kuvomereza ma ukwati otere.

A Papa anatinso anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha ndi ana a Mulungu ndipo ali ndi ufulu okhala pa banja.

Malingana ndi a Papa, mpingo ukuyenera kupanga njira zovomerezera ma ukwati otere  kuti maukwatiwa akapangidwa azikhala ovomerezeka ndi malamulo.

Zomwe wanena Papazi zikutsutsana ndi zomwe mpingo wa Katolika ku Malawi umanena nthawi ndi nthawi kuti kugonana amuna kapena akazi okhaokha sikololedwa chifukwa ukwati umayenera ukhale pakati pa mkazi ndi mamuna basi.

Wansembe a Montfort Sitima adanena chaka chatha kuti amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha ndi osokonekera ubongo ndi ofunika chikondi ndi chisamaliro.

Ku Malawi Malamulo salola kukwatirana amuna kape akazi okhaokha.

 

Advertisement