Yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino posachedwapa a Everton Chimulirenji ati anthu asaloze chala mtsogoleri wa dziko lino pakuchotsedwa kwawo pa mpando poti anawachotsa pampandowu ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM a Saulos Chilima.
A Chimulirenji amayankhula izi lachinayi ku Mayani m’boma la Dedza pomwe anali ndi misonkhano yoyimayima limodzi ndi mtsogoleri wa chipani cha UDF a Atupele Muluzi.
Iwo anati anthu asamaloze chala a Muluzi kuti ndi omwe anapangitsa kuti iwo achoke pampando wa wachiwiri kwa mtsogoleri ndipo ati anthu aziloza chala a Chilima kaamba koti ndiomwe anapita kukamang’ala kukhothi kuti zisankho sizinayende bwino.
Mkuluyu watsindikaso kuti ubale wawo ndi mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika uli bwinobwino ndipo anthu asaganize kuti pali udani potsatira kusankhidwa kwa a Muluzi kukhala otsatira wa a Mutharika pachisankho chikubwerachi.
“Anandichotsa pa mpando wa vayisi pulezidenti (vice president) si Atupele Muluzi. Amene anandichotsa ine pampandowu ndamene anagwirizana ndi anthu ndikupita ku khothi kukatsekula mlandu ine nkupezeka kuti sindili pamenepo.
“Ndipo akupita pansonkhano ndikumanena kuti a Dzonzi amayambana ndi anthu ndichifukwa chake anawachotsa nkuika a Muluzi, nanga a Dzonzi amayambana ndi anthu? Anandichotsa ndiiwowo asamaname adzikhala ndi manyazi.” anatero Chimulirenji.
Poyankhula pa msonkhano omwewu, a Muluzi anati anthu avotele mgwirizano wa zipani za DPP ndi UDF ndipo ati uwu ndi mgwirizano okhawo omwe ungabweretse chitukuko chenicheni m’dziko muno.
Apa a Muluzi anati mgwirizanowu ukalowa m’boma udzaonetsetsa kuti magetsi komaso zitukuko zina zifikile m’madera akumidzi omwe nthawi zambiri amasalidwa pankhani ya chitukuko.
Pakadali pano, bungwe la MEC, mlangizi wa boma pankhani ya za malamulo a Kalekeni Kaphale ndiso komiti yakunyumba yamalamulo pankhani ya zamalamulo agwirizana kuti chisankho chichitike pa 23 June, 2020 osatiso pa 2 July monga linanenela bungwe la MEC m’mbuyomu.