Abale samalani: Manyi aja abweranso mu Lilongwe

Advertisement

Nkutheka kuti inu simunamwepo koma mwina azanu munakhisana nawo aja anamwapo. Madzi atubvi la khatikhati anavuta ku Lilongwe aja atulukiranso.

Pano ndiye adza ndi ukali, kununkha kwakeko ndiye ngati wangowatunga mu suweji madziwa kuti umwe. Ena nkumati awa si madzi a manyi ai, koma manyi a madzi, zomwe zapangitsa mkulu wa Lilongwe Water Board, lomwe ndi bungwe logawa madzi mu Mzindawu kuopseza kuti lisiya ku pereka madzi mu madera ena.

Mkuluyu anayankhula izi atazazidwa ndi ukali kwinaku akunyogodola bungwe lazanyumba (Malawi Housing Corporation) lomwe ati likukanika kuti liyambira pati kuti lithetse vuto la manyili.

Malipoti omwe atipeza ndi oti vutoli lakhudza kwambiri dela lomwelija la Area 18. Ngakhale izi zili chomwechi, anthu ambiri mumadera ena mu Lilongwe akuopa kumwa madzi.

Advertisement

23 Comments

  1. This is the second time right? What else do we expect from the now government? And you Waterboarding body…team off assholes.

  2. A Malawi kulakwa kumeneko, zowona kuphwasula Dala ma Pipe ndi cholinga chofuna kuwononga Mbiri ya Boma. Yehova akukuwonani.

  3. Koma masiku ano. madzi odura koma ali wochokela ku chimbudzi. koma vutoli lidzathadi? kwatsalano kuti timwe madzi amix magazi tsopano.tiziwona.

  4. Kkkkkkkkkkk Malawi24 tsopano!! Auzeni masapota a DPP wo kuti boma lawo likuchita chothekera kumwetsa anthu manyi.

Comments are closed.