Atchola banki lalikulu lero asilikali a ku Zomba pamene anzawo a ku Kaning’ina abetsa mifuti kwa nyerere zomwe zawatimba pakwawo pomwe.
Amene anati ligi ndi kumadzulo analinga ataona ndithu, ma Bankala atakhala pachiwiri kwa nthawi ndithu, achotsedwapo lero ndi maule.
Pa masewelo amene anachitika lero, asilikali a ku Zomba a Red Lions aonetsa mbonaona timu ya Siliva ataithibula ndi zigoli ziwiri kwa duuu!
Mnyamata Chimwemwe Chidati ndiye anathila onga otchola zitseko za ku banki lalikulu mu chigawo chachiwiri.
Pamene asilikali a ku Zomba anagwilitsa mwa luso mfuti zawo kuti adzetse chimwemwe kwa owatsatila, anzawo ku Mzuzu anali kuodzela mpaka abeledwa mifuti ndi nyerere.
Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la Mzuzu, anyamata a noma anaonetsetsa kuti abwenze chipongwe chimene asilikali a ku Kaning’ina anaonetsa powatulutsa mu chikho cha FISD.
Zigoli za anyamata atatu amene dzulo anakanika kuona golo ku Karonga ndizo zayandamitsa timu ya Moyale.
Precious Sambani, Essau Kanyenda ndi Khumbo Ng’ambi ndiwo anakhoma asilikali a ku Kaning’ina pakwawo pomwe. Mnyamata Chamveka Gwetsani anangoponyamo ka chipukuta misonzi basi.
Pa masewelo ena, timu ya Bullets yachapa timu ya Blue Eagles ndi zigoli zitatu kwa duuu ku Blantyre kuti iyo ikatenge malo a wachiwili mu ligi podomola Siliva.
Zotsatila zonse za masewelo lero zinali motele:
Moyale barracks 1-3 Beforward Wanderers
Mafco 2-1 Mzuni
Masters security 2-0 Dwangwa United
Red Lions 2-0 Silver Strikers
Big Bullets 3-0 Blue Eagles
Tsogolo La Maule Lokhala Pa # 2 Lili Mmanja Mwa Manoma Ma Banker Osadandaula Mukweraxo Pa 2
Nyerere zmanoma kp de fire burning moto umapta kwasala tchre”””
noma ndi timu yanga 4 life n tazakhala ndi dolla zaimangira stadium
Noma woyeee %
Kkkkkkkkkkkkkk
hello everyone am happy sharing this with you, am not suppose to be doing this but i can’t hold back my joy so i have to share with you, you too can be help just as i was helped by Dr Odudu who cured me the HIV virus after suffering from it for some years and CD4 count was very low i was depressed, i was desperately in need of getting rid of it, but the ARVs were not helping so i was eager to contact Dr Odudu who gave me his herbal medicine, today as am posting this i am HIV negative, don’t hide your sickness or else your sickness will hide you, contact Dr Odudu today so that you see a reason to back through the years of your depression and smile to yourself, you can call or whatsap him with his number (+2349067902914)or email [email protected] , pardon me i offend you with this post, but i must share this good news
Kkkkk
It is Red Lions 1 Silver 0…… and Not Red Lions 2 Silver 0. achitsiru a reporter mukungoonetsa u fanaticism wanu ndi Nyasa Bullets. Ndi zampira izi, osathamanga mwazi.
Ngati ma banker anakukasulani mu tnm League, komanso kukugudumutsani mu Airtel top 8, ikhale chifukwa coponyera mabodza?
Zilemban Osatenga Mbali Noma Ikaluza Mmalemba Zambir Ngat Kwacha Yagwa Ndpo Mafuta Akwera
Nyerere zazikulu
Lelo mwayankhula mokondwa chifukwa team yanu ili pa position 2
Silver For Life Sindikujejemaso Ata Mawa Ndinu Muliranso
VoFiiiiiRaaaaa………vafika ntauniii…….NKHAWAaaa Biiiiiiiiiii………Ligiii ife manoma titenga komaaa??? Vimatizunza ivi bwanji…
ma bankala zavuta
Noma ndidiru osatizinazi,wamkaka tisambezimenezi..
Mbuzi Ya munthu Demeti. Iwe Admin Ikaluza Wonderers Umalemba Zosambwaza Kwambili Koma Apa Ena Sizinawayendele Sunalembe Ngati mene Umalembela Ikhala Wonderers Yaluza
Kuli nyerere wooooooooooooooooeee
ndikasapote bullets ngati chitsilu ayiiiiii ndithu
vafika vofiiraaa…….NKHAWA Biiiiiii
upsa mtima tili pambuyo pako maulle samala
You mean World Bank has been robbed? Hey how much dollars? These thieves are billionaires,
Noma yawina eti? eee! mmene ndapsela mtimamo
manoma woye!!! kwasala kwamawa
team ya anthu oganiza bwino
nyerere ndmoo
unproffesion writing please improve ur way of writng
to it is sounding gud ZA u professional sixikumakoma
chi team noma komweko akanene!!!!!!
kuchoka ku Lilongwe kupita ku Bt Kuzatenga 1point
Anayamba ndi maple kupita ku mpoto kukatenga 1point mu first round,Noma kuti woyeeeeee
Kubanja la NOMA chimwemwe basi.
Bankers ipanga bounce back….anyamata pressure ya unbeaten run inawakulira..adzukanso
i kakhala ndudu ya 2010 yo, nyerere ziperapera zokha ndikuyiyika pa soft kachikena
Eeeeee MOYALE ndi manyakaaaaa
umagoziwilatu apswe mtima zenin*2 zikuwawawo ife ndi noma basi
It Hapenz
Zimenezo ndie nyerere lig njake
well said
Wefu wefu wake ameneyu!