Palibepo pachiwiri paja Bankala, ndipo nyerere zabwenza chipongwe kwa Moyale

Advertisement
Super League Malawi

Atchola banki lalikulu lero asilikali a ku Zomba pamene anzawo a ku Kaning’ina abetsa mifuti kwa nyerere zomwe zawatimba pakwawo pomwe.

Amene anati ligi ndi kumadzulo analinga ataona ndithu, ma Bankala atakhala pachiwiri kwa nthawi ndithu, achotsedwapo lero ndi maule.

Super League Malawi
Manoma Kusangalala

Pa masewelo amene anachitika lero, asilikali a ku Zomba a Red Lions aonetsa mbonaona timu ya Siliva ataithibula ndi zigoli ziwiri kwa duuu!

Mnyamata Chimwemwe Chidati ndiye anathila onga otchola zitseko za ku banki lalikulu mu chigawo chachiwiri.

Pamene asilikali a ku Zomba anagwilitsa mwa luso mfuti zawo kuti adzetse chimwemwe kwa owatsatila, anzawo ku Mzuzu anali kuodzela mpaka abeledwa mifuti ndi nyerere.

Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la Mzuzu, anyamata a noma anaonetsetsa kuti abwenze chipongwe chimene asilikali a ku Kaning’ina anaonetsa powatulutsa mu chikho cha FISD.

Zigoli za anyamata atatu amene dzulo anakanika kuona golo ku Karonga ndizo zayandamitsa timu ya Moyale.

Precious Sambani, Essau Kanyenda ndi Khumbo Ng’ambi ndiwo anakhoma asilikali a ku Kaning’ina pakwawo pomwe. Mnyamata Chamveka Gwetsani anangoponyamo ka chipukuta misonzi basi.

Pa masewelo ena, timu ya Bullets yachapa timu ya Blue Eagles ndi zigoli zitatu kwa duuu ku Blantyre kuti iyo ikatenge malo a wachiwili mu ligi podomola Siliva.

Zotsatila zonse za masewelo lero zinali motele:

 

Moyale barracks 1-3 Beforward Wanderers
Mafco 2-1 Mzuni
Masters security 2-0 Dwangwa United
Red Lions 2-0 Silver Strikers
Big Bullets 3-0 Blue Eagles

 

 

Advertisement

40 Comments

  1. hello everyone am happy sharing this with you, am not suppose to be doing this but i can’t hold back my joy so i have to share with you, you too can be help just as i was helped by Dr Odudu who cured me the HIV virus after suffering from it for some years and CD4 count was very low i was depressed, i was desperately in need of getting rid of it, but the ARVs were not helping so i was eager to contact Dr Odudu who gave me his herbal medicine, today as am posting this i am HIV negative, don’t hide your sickness or else your sickness will hide you, contact Dr Odudu today so that you see a reason to back through the years of your depression and smile to yourself, you can call or whatsap him with his number (+2349067902914)or email drodudu[email protected] , pardon me i offend you with this post, but i must share this good news

  2. It is Red Lions 1 Silver 0…… and Not Red Lions 2 Silver 0. achitsiru a reporter mukungoonetsa u fanaticism wanu ndi Nyasa Bullets. Ndi zampira izi, osathamanga mwazi.
    Ngati ma banker anakukasulani mu tnm League, komanso kukugudumutsani mu Airtel top 8, ikhale chifukwa coponyera mabodza?

  3. VoFiiiiiRaaaaa………vafika ntauniii…….NKHAWAaaa Biiiiiiiiiii………Ligiii ife manoma titenga komaaa??? Vimatizunza ivi bwanji…

  4. Mbuzi Ya munthu Demeti. Iwe Admin Ikaluza Wonderers Umalemba Zosambwaza Kwambili Koma Apa Ena Sizinawayendele Sunalembe Ngati mene Umalembela Ikhala Wonderers Yaluza

Comments are closed.