Majenereta akabwezedwe, magetsi atsike mtengo

Advertisement
55 MW generators Malawi

Bungwe lowona za ufulu wa anthu ogula katundu m’dziko muno lapempha bungwe logulitsa magetsi la Escom kuti litsitse mtengo wa magetsi.

Wapeleka pempholi ndimkulu wa bungwe la Consumers Association of Malawi (CAMA) a John Kapito omwe ati boma kudzera ku bungwe la Escom likuyenera mwanjira iliyose litsitse mtengo wa magetsi omwe ati ndiokwera kwambiri.

Chaka Chatha, Bungwe logulitsa magetsi la Escom linabwereka ma jenereta opangira magetsi kuchokera ku kampani yobweleketsa ma jenereta ya Aggreko.

Izi zinali kaamba ka vuto lakuzimazima kwamagetsi lomwe linafika povuta kwambiri mchakachi ndipo kubwerekedwa kwa majeneretawa kunapangitsa kuti mitengo ya magetsi ikwezedwe zomwe zinadandaulitsa a Malawi ochuluka.

Koma pakadali pano, ngakhale kuti Escom inasiya kugwiritsa ntchito majeneletawa, bungweli likumapelekebe ndalama ku kampani ya Aggreko zomwe zikupangitsa kuti mtengo wa magetsi ukhalebe okwera.

Poyankhulapo pankhaniyi, wapampando wa bungwe lowana za anthu ogula komaso kugulitsa katundu la Consumers Association of Malawi a John Kapito ati Escom ikuyenera mwanjira iliyose itsitse mtengo wa magetsiwu.

A Kapito ati bungweli likuyenera kutsitsa mtengowu kaamba koti pakadali pano silikugwiritsa ntchito ma generetawo ndipo auza boma kuti likabweze ma generetawa ponena kuti silikuenera kumalipila ndalama zambiri mbiri pomwe katunduyu sakugwiritsidwa ntchito.

“Pakadali panopa magetsi tili nawo okwanira koma paja kuli nkhani ya renti ya majeneleta. Nde ife tikuti bwanji osangotenga majeneletawo mkubweza kwa eni take kusiyana mkuti iwowo apeleke chipsinjo kwaife anthu amene timagwiritsa ntchito magetsi.

“Chifukwa pakadali panopa magetsi anakwera kwambiri chifukwa chogwiritsa ntchito majeneleta amenewawa omwe pano sakugwira ntchito. Chimene timafuna ife mchoti majenereta amenewa abwelere, adzipita kwawo.” Watelo Kapito.

Iwo ati ngati magetsi angazayambileso kuvuta mtsogolomu ndikwabwino kuti boma lizapeze njira zina zotchipilako kuyelekeza ndima jeneretawa omwe ati akhala chipsinjo pa anthu omwe amagwiritsa ntchito magetsi mdziko muno.

Advertisement

One Comment

  1. Ndizomvetsa chisoni kuti anthu amene akuti ndi omenyera mawufuluwa nthawi zina akumapereka uthenga osokoneza amalawi ngati ndife osazindikira. Zomwe zikunenedwa apa ndi zosatheka. Ndani Sadziwa kuti muthu umapanga busines kuti upindule molingana ndi ndalama zomwe udawononga pokhazikitsa busineziyo komaso zokonzetsera, ndi zina. Chonde thawi iyi ndi ya khani ya zisakho musanene izi kuti mutchuke….lnu nomwe mukufuna IPP inuso mukuti magetsi atsike …ndani IPP angabwere kudzamaluza kunoko…nenani zowona…magetsi sangatsike…magenereta sangabwezedwe…capacity yanthu yamagetsi ndiyochepa kwambiri…pangani kafukufuku tiwone. Panopa ngati Malawi timayenera kukhala ndi 800MW koma tili mma400MW kuphatikiza ma renewable…ndiye magenereta achoke ….ndiye tipita patipo…zosatheka…

Comments are closed.