…kuthimathima kwamagetsi ikhala mbiri…
Mtsogoleri wa dziko lino Arthur Peter Mutharika wati akwaniritsa zonse zomwe wakhala akulonjeza nthawi yokopa anthu koma walimbikitsa umodzi ndi chikondi kuti dziko lino litukuke.
A Mutharika amayankhula izi lachisanu m’mawa pa bwalo lamasewero la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre pamwambo owakhazikitsa kukhala mtsogoleri wa dziko lino potsatira kupambana kwawo pa zisankho zapitazi.
Iwo anati ali okondwa kuti a Malawi ochuluka anawasankha iwo ndipo alonjeza kuti atukula dziko lino koma apempha kulolerana ndinso mgwirizano.
Poyankhula kukhwimbi la anthu omwe anasonkhana pa mwambowu, a Mutharika anati kusankhidwa kwawo ndichisonyezo choti amalawi akufunadi dziko lino litukuke ponena kuti iwo ndikazembe wa chitukuko.
Iwo anati ndi mtsogoleri wa anthu onse posatengera kuti anawavotera kapena ayi komanso posayang’anira chigawo, chipembedzo komaso mtundu ndipo apempha kugwirana manja kuti dziko lino lipite chisogolo pankhani ya chitukuko.
Mtsogoleri wadziko linoyu analimbikitsaso anthu mdziko muno kuti apitilire kusunga bata nthawi zonse ponena kuti nkhondo siimanga mudzi ndipo dziko silingapite chitsogolo ndi mikangano kapenaso kukhetsa mwanzi.
Iwo anadzudzulaso amabungwe kaamba kosabwera poyera ndikudzudzula pomwe anthu ochuluka a chipani chawo cha DPP akhala akuchitilidwa nkhanza ndipo anawapempha kuti asinthe ndicholinga choti pakhale mgwirizano pankhani yotukula dziko lino.
Pankhani yokhudza chitukuko, a Mutharika alonjeza kuti akwanilitsa zonse zomwe akhala akulonkeza panthawi yokopa anthu ndipo mwazina ati aonetsetsa kuti chuma chadziko lino chipitilire kupita pa tsogolo.
“Ndachita zinthu zochuluka pazaka zisanu zapitazi kupambana maboma onse omwe akhalapo mmbuyomu mumbiri ya dziko lino ndipo zaka zisanu zina zikubwerazi ndichitasa zochuluka ndipo ndiika patsogolo nkhani yopanga zinthu zosiyanasiyana.
“Vuto lathu lalikulu mudziko mwathu muno lakhala kuthimathima kwa magetsi, koma tsopano tikuthetseratu vutoli ndipo amalawi onse atsazikane nawo mdima mpaka kalekale,” anatero Mutharika.
A Mutharika anatiso boma lawo pazaka zisanu zimenezi lipeleka mwayi wantchito kwa achinyamata ochuluka komaso kuti apitiliza ndi ndondomeko yomanga sukulu zophuzilira ntchito za Manja kuti achinyamata omwe sanapite patali ndi maphuzilo awo apeze chochita.
Ena mwa anthu odziwika omwe anafika kumwambowu ndi yemwe anali mtsogoleri wadziko lino a Bakili Muluzi, komaso ena omwe amaimilira maiko osiyana siyana monga; Tanzania, Zimbabwe, Mozambique, Zambia, Eswatini.