Tiwonetsetsa kuti chilungamo chidziwike pa imfa ya Chilima, watelo Kabambe

Advertisement
UTM

Yemwe wangosankhidwa posachedwapa ngati mtsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) Dalitso Kabambe, watsindika kuti chipanichi chikutsatira mwachidwi kafukufuku wa ngozi ya ndege yomwe idapha malemu Saulos Chilima komaso ena asanu ndi atatu.

Kabambe wayankhula izi Lolemba pomwe pamodzi ndi akuluakulu ena achipani cha UTM anapita ku phili la Nthungwa, m’nkhalango ya Chikangawa pa malo amene thupi la malemu Chilima lidapezekera itachitika ngoziyi pa 10 June, 2024.

Poyankhula pa malowa, Kabambe wati: “Munthu amene waona chigawenga chikuwombela m’bale wake, amavala udindo ofuna kudziwa kuti chinachitika ndi chiyani. Ifeyo ngati atsogoleri a UTM titenga udindo oti tidziwe kuti chinapha m’bale wathu, mtsogoleri wathu ndi chiyani. Pamodzi tidalonjeza kuti tipanga zimenezi.

Kuwonjezera apo, Kabambe walonjeza kuti chipani cha UTM sichilora kuti banja la malemu Chilima liyende lokha, ndipo watsindika kuti chipanich chiyesetsa kuti banjali likukhala mwa ufulu.

Iye wapemphaso boma kuti limange chikwangwani cha chikumbutso pa malo angoziwo. “Ndipemphe boma kuti limange chikwangwani chachikumbutso pano, osati chomwe chilipanochi.”

Ena mwa adindo amene anali nawo pa ulendowu ndi monga nsungi chuma wa chipanichi Olipa Muyawa, woyang’anira ntchito yokopa anthu Maqwenda Chunga, woyang’anira achinyamata Penjani “Fredokiss” Kalua komanso ma membala ena achipanichi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.