MV Chambo ikuyambiranso maulendo ake pa nyanja ya Malawi

Advertisement
Likoma

Anthu okhala pa zilumba za Likoma ndi Chizumulu akhala ndi mwayi wa mayendedwe osavuta kufika komanso kuchoka ku Nkhata-Bay ndi madera ena, kaamba koti unduna wa zamayendedwe walengeza kuti sitima ya MV Chambo yomwe idalembetsedwa mukaundula wa sitima za m’dziko la Mozambique, iyambiranso kuyenda pa nyanja ya Malawi.

Wofalitsa nkhani mu Undunawu, Watson Maingo, wati sitima ya MV Chambo iyamba maulendo ake pa 26 September, 2024, zomwe zichepetse mavuto amayendedwe pa nyanja ya Malawi.

Maingo wati MV Chambo yomwe imathandiza anthu kuyenda panyanjayi mosavuta, idayima kaye muchaka cha 2019 chifukwa cha mliri wa Covid-19 pomwe malire a dziko lino ndi Mozambique adatsekedwa kaye.

Wapampando wa komiti yachitukuko m’dera la kumpoto kwa Likoma, Frank Mkali wati kubwera kwa MV Chambo kudzetsa mpumulo kwa anthu a pazilumbazi kuphatikizapo anthu ogwira ntchito zosiyanasiyana.

“Ndizomvetsa chisoni kuti anthu ena akulephera kuyenda bwino chifukwa anavulala polimbirana kukwera sitima chifukwa cha kuchulukana kwa katundu ndipo ena akhala akutaya katundu wawo,” wadandaula Mkali.

Iye adaonjeza kuti anthu ena akhala akukana ntchito ku Likoma chifukwa cha mavuto omwe amakumana nawo pamadzi, zomwe ati zasokoneza anthu ogwira ntchito pachilumbachi.

Posachedwapa mabungwe osiyanasiyana akhala akupempha boma kuti lilowererepo powonjezera zombo zina pa nyanja ya Malawi kuti zichepetse mavuto a mayendedwe apamadzi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.