Ndinabeledwa chisankho mu 2019 – wadandaula Kaliati

Advertisement
Patricia Kaliati

Patricia Kaliati yemwe ndi mlembi wankulu wa chipani cha United Transformation Movement (UTM), wati adawina chisankho cha phungu wa nyumba ya malamulo mu 2019 koma adabeledwa, ndipo wati sadafune kuyikoka nkhaniyi.

Kaliati yemwe amayankhula izi lachinayi madzulo mu pologalamu ya padera yomwe idawulutsidwa pa wayilesi ya Zodiak, wati ali ndi umboni ogwilika za nkhaniyi.

Iwo ati, “Kulephera kwa ine ku derako sikunali koti anthu sanandifune koma sindinafune kuti ndiwatengere ku khothi. Ndinawina koma sindinafune kuwatengera anthu ku khothi kuti ndiwawonetse kuti alakwitsa.

“Ineyo ndinawina ndipo ku UTM kuli anthu ambiri omwe anawina chisankho cha 2019 koma sanafune kuchitapo kanthu. Ndinayamba kale kuti ndiitengere ku khothi. Panopa ndi pomwe zikuwululika. Bungwe la MEC litha kukhala mboni yanga chifukwa kuli anthu omwe amatiuza momwe zimakhalira.”

Iye wati amakhulupilira kuti pali anthu ena omwe samamufunira zabwino ndipo ndi omwe anapanga upo kuti iwo abeledwe chisankhocho.

Pa chisankho cha mchaka cha 2019 kudera la kum’mawa kwa boma la Mulanje, Yesuf Nthenda wachipani cha DPP. anagonjetsa a Kaliati pamodzi ndi anayi ena omwe amapikisana pa udindo wa phungu wa nyumba ya malamulo.

Advertisement