Nsanje ndi matenda, wapha mkazi wake ndi nkhwangwa 

Advertisement
Lilongwe

Bambo wina wazaka 42, ku Lilongwe wakadzipereka yekha m’manja mwa apolisi ku Area 3, atakhapa ndi kupha mkazi wake ndi nkhwangwa atazindikira kuti mkaziyo akuzemberana ndi njonda ina.

Mneneli wa apolisi ku Lilongwe, a Hastings Chigalu watsimikiza zankhaniyi ndipo wati bamboyu dzina lake ndi Isaac Patisi ndipo wakhapa mkazi wake wazaka 36, Azefa Kasamanda.

Malingana ndi a Chigalu ati mamunayu anayambana ndi mkazi wakeyu atazindikikira kuti mkaziyu akumayenda ndi mamuna wina mwanseli.

Mkangano utakula bamboyu anakhapa mkazi wakeyu ndi nkhwangwa pa chifuwa ndikuthawa atazindikira kuti yalakwa.

Koma asanakadzipere ku polisi, iye anakamufotokozera mchemwali wake zaupanduzi.

A Chigalu ati bamboyu wachita izi ku Malingunde komwe amakhala ndi mkazi wakeyo.

Bamboyu amachokera m’mudzi mwa mwa Chakulirapati, kwa mfumu yaikulu Masumbankhunda ku Lilongwe, ndipo akuyembekezeka kukayankha mlandu wakupha.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.