Chakwera ayankhanso Mutharika: ulamuliro wanga wakumana ndi zokhoma zambiri ndi chifukwa ndalephera

Advertisement
President Lazarus Chakwera

Iyi ithera ku waya ndithu. Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera akuoneka kuti sanathane ndi moto omwe owatsutsa a Peter Mutharika adayatsa ku Blantyre lamulungu lapitali pa msonkhano wawo wandale. Adakapitiriza kuwayankha mokuluwika.

Lero lachinayi a Chakwera adzudzula atsogoleri omwe akupitiriza kuwanena kuti ndiolephera. Iwo anena izi mu mzinda wa Lilongwe. A Chakwera ati atsogoleri oterewa angofuna kunyengeza a Malawi kamba koti ulamuliro wawo udafikila pa mpeni.

Mwa zina, a Chakwera adafotokozapo kuti nkhondo ya pakati pa maiko a Russia ndi Ukraine ndiyomwe yapangitsa kuti zinthu zisokonekere mu dziko muno. Iwo adaonjezeraponso kuti namondwe amene dziko lino adakumana naye adangosokonezeratu ndondomeko zawo za chitukuko.

Zokamba za a Chakwera zabwera pamene a Mutharika adauza namtindi wa anthu ku Njamba kuti a Chakwera akulephera monga iwo adachenjezera a Malawi nthawi ya kampeni. A Mutharika akhala akunena mobwelezabweleza kuti zinthu mu dziko muno zakwera chifukwa cha a Chakwera.

Pa msonkhano wawo omwewo, a Mutharika adanena mochilimika kuti pakatha zaka ziwiri zokha iwo adzakonza zinthu mu dziko muno. Iwo adati adzachita monga adachitira mu chaka cha 2014 pamene adatenga boma kwa a Joyce Banda.

Izi ndi chifukwa zikuoneka kuti kuyankhula kwa a Chakwera lero akupitiriza kuyankha a Mutharika. Pachiwiri, a Chakwera adali mu mzinda wa Blantyre komwe adayankhulakonso mozembelera kunena a Mutharika kuti salowanso m’boma.

Anthu ochuluka akhala akudandaula ndi utsogoleri wa a Chakwera kunena kuti zinthu zakwera mitengo ndipo zinthu zochuluka nazo zakhala zikusowa mu dziko muno. Izi ndi monga suga, pena mafuta komanso ziphaso zoyendera.

Advertisement