Chiwerengero cha anthu omwalira ndi ‘ambuye mtengeni’ chafika pa 8

Advertisement

Ofesi ya zaumoyo munzinda wa Blantyre yati chiwerengero cha anthu omwe afa m’dera la Manase kamba komwa mowa osadziwika bwino omwe ukutchedwa ‘ambuye mtengeni’ kapena kuti ‘magagada’, chafika pa asanu ndi atatu (8).

Izi ndi malingana ndi ofalitsa nkhani ku ofesi ya zaumoyo mu nzindawu a Chrissy Banda omwe ati kukwera kwa chiwerengeroku kukutsatira kumwalira kwa munthu wina m’mawa wa Lolemba pa 8 April, 2024.

Anthuwa akuti anamwa mowa osakhala bwinowu sabata latha ndipo Loweluka pa 6 April, 2024, chiwerengero cha anthu omwe anamwalira chinali chili pa isanu ndi m’modzi ndipo Lamulungu munthu winaso m’modzi anamwalira akulandira thandizo la mankhwala ku chipatala cha Queen Elizabeth ku Blantyre komweko.

Lolemba, ofesi ya zaumoyoyi yati munthu m’modzi mwa anthu awiri omwe anagonekedwa munchipinda cha anthu odwalika kwambiri, ndiyemwe wamwalira zomwe zapangitsa kuti chiwerengerochi chikwere kufika pa 8.

Pakadali pano munthu m’modzi akulandirabe thandizo la mankhwala munchipinda cha anthu odwalika kwambiri pa chipatalachi.

Lamulungu lapitali, ofesi ya zaumoyoyi inatulutsa zotsatira za kupimidwa kwa matupi a anthu omwe atisiyawa zomwe zasonyeza kuti mowa omwe anthuwa anamwa munali poyizoni.

Potsatira izi, apolisi munzindawu amanga anthu angapo omwe akukhudzidwa ndi kufulura mowa wa ‘ambuye mtengeni’

Advertisement