Ma Membala a PAC apewe kulandira ma udindo kuchokera kwa mtsogoleri wa dziko

Advertisement
Dinala Chabulika

Woyankhulira chipembedzo cha chisilamu Sheikh Dinala Chabulika wati dziko lino likumagawanika chifukwa cha mipingo maka ikaonetsa chidwi pa amene anthu akhonza kudzamsankha pa masankho a mtsogoleri wa dziko ndipo ati nthawi yakwana tsopano kuti atsogoleri a bungwe la Public affairs Committee (PAC) asamalandile ma udindo kuchokera kwa mtsogoleri wa dziko.

Poyankhula lero mu pologamu ya Kulinji pa wailesi ya Times, A Chabulika ati zochitika za mipingo kusankhiratu munthu mwa kabisila zimasokoneza mipingo komanso onse otsatila maka pamene chisankho cha atsogoleri chayandikira ndipo ayamikira makalata amene mipingo imalemba ponena kuti amathandiza kwambiri atsogoleri adziko ndi owatsatira kuti adzitenga nzeru.

Sheikh Chabulika ati ma udindo amene atsogoleri a bungwe la zipembedzo la PAC amakhala nawo mu ma board a mabungwe a boma kumasokoneza mmene angadzudzulire mtsogoleri wa dziko ndi nduna zake.

“Ndipo ndipemphe kuti mwina ku PAC tisiye kulandila ma udindo kuchokera kwa president Chifukwa three quarters ya ambiri a PAC ndi ma board membala a ma company a boma ndipo tikugulidwa kwambiri ndipo zimakhala zovuta kuluma dzanja lomwe likukudyetsa” anatero a Chabulika.

Wa pampando wa bungwe la PAC monsignor father Patrick Thawale anavomeleza kuti mzofunika kuziunika kwambiri za ma udindo a atsogoleri a PAC ndipo anayamika a Chabulika, ponena kuti msonkhano wa PAC ukubwera kutsogoloku akuyenera adzayikambilane nkhaniyi.

M’modzi mwa omenyera ufulu mdziko muno a Micheal Kaiyatsa ati sizoyenera kuti atsogoleri adzisankha amene anthu adzamvotere ndipo izi ndi zokupha ufulu wa owatsatila pa ndale.

A kaiyatsa ati dziko likuyenera kulingalira kukhala ndi lamulo lokaniza atsogoleri a mipingo kuwakaniza kusankhilatu mtsogoleri amene anthu adzamsankhe.

Advertisement