Apolisi ku Kasungu apempha anthu oyendetsa galimoto kuti ‘ ‘asayiponde fadah’ komanso asayendetse atapapira bibida komanso mankhwala ozunguza bongo pofuna kuti aliyense alowe mchaka chatsopano cha 2024 ndi moyo.
Yemwe ndi komishonala wa apolisi mchigawo chapakati ku m’mawa a Rhoda Manjolo ndi omwe ayankhula izi kumadyelero omwe amachitikira pa sukulu ya sekondale ya Loyola m’bomali.
Iwo anapitilizanso kufotokoza kuti ndi ntchito ya apolisi kuonetsetsa kuti anthu mdziko muno ali otetezeka ndipo aliyense walowa mchaka cha 2024 ali ndi moyo.
Imfa za ngozi zapamsewu zimachuluka maka munyengo ino yazisangalalo, kotero anthu akuyenera kukhala osamala kuti tipewe.
Masiku apitawa, anyamata ena anazijambula akuthamangitsa galimoto lawo ku Zomba. Anyamata omwe anakwera mu galimotomo amachita kuwuza oyendetsa kuti “ipondeni fada”. Masewera awowa anathera pakona pomwe galimoto inakanika kukhota ndipo inasiya msewu ndikukathela mu dothi. Malipoti akuti anthuwa apulumuka koma apolisi sanayankhulepo pa ngoziyi.