Ka peanut? K93 miliyoni ikufunika yokozera zomwe ophunzira pa Mzuni anawononga

Advertisement
Mzuzu University students in September held protests and damaged various property including this signpost

…chikwangwani cha polisi chikufunika K350,000

Nkhonya yobwezera kuwawa; ophunzira pa sukulu ya ukachenjede ya Mzuni nkhawa ili bii pomwe za dziwika kuti ndalama yokwana K93 miliyoni ndi yomwe ifunike pa ntchito yobwezeretsa zinthu zomwe zinawonongeka pa ziwonetsero mwezi watha.

Pa 15 September chaka chino, ophunzira pa sukuluyi anachita ziwonetsero atakanika kuvana chichewa ndi akuluakulu oyendetsa sukuluyi pa kukwezedwa kwa ndalama yomwe amalipira (fizi).

Ophunzirawa anati anali odabwa kuti akuluakulu oyendetsa sukulu ya Mzuni anapanga chiganizo chokweza fizi chaka cha sukulu chidakali pakati.

Ophunzirawa anayamba kuchita ziwonetsero ndipo mwa zina anatseka misewu komaso kuwononga katundu osiyanasiyana zomwe zinapangitsa kuti akuluakulu a sukuluyi atseke sukuluyi ndipo analamula ophunzira onse kuti achoke pasukuluyi m’mawa wa pa 16 September, 2023.

Potsatira nkhaniyi, akuluakulu a sukulu ya Mzuni, nthambi yowona za misewu komaso gulu la anthu ochita malonda pa nsika wa Luwinga, anachita kafukufuku ofuna kupeza chiwerengero cha katundu yemwe anawonongedwa pa ziwonetserozi.

Kafukufuku wa akuluakuluwa wapeza kuti pakufunika ndalama yosachepera 93 miliyoni kwacha yoti igwire ntchito kubwezeretsa katundu yese amene ophunzira pa sukuluyi anawononga pa ziwonetserozo.

Mwa zina akuluakuluwa ati anthu ochita malonda pa nsika wa Luwinga akufuna ndalama yokwana 46.8 miliyoni kwacha kuti abwezeretse katundu wawo yemwe anawonongeka komanso 28 miliyoni kwacha yowapepesa chifukwa cha kupsinjika maganizo.

Akuluakuluwa ati bungwe la Roads Authority likufuna ndalama zokwana MK5.3 miliyoni zokonza msewu wa M1 omwe unawonongedwa pamene kampani ya China State Construction ikufuna ndalama zokwana MK11.3 miliyoni kuti iwonjezere nthawi ya polojekiti yake potsatira kusokonezedwa.

Mbali inayi sukulu ya Mzuni payokha ikufuna MK2 miliyoni kuti igwire ntchito yobwezeretsera matayala agalimoto omwe anatengedwa m’malo omwe mukuchitika mapolojekiti osiyanasiyana.

Zadziwikaso kuti chikwangwani cha polisi ya Luwinga chomwe chinazulidwa chikufunika ndalama yokwana MK350,000 kuti chibwezeretsedwe pa malo pomwe chinali.

Pakadali pano sizinadziwike kuti ndalama imeneyi ichokera pati koma pali mphekesera yoti ophunzira onse pa sukuluyi ndi amene akuyenera kusonkherana.

Advertisement