Aphungu awonetsa kukhudzika ndi umphawi msukulu za dziko lino

Advertisement
Ben Kondowe and other officials from Civil Society Education Coalition (CSEC)

Aphungu anyumba yamalamulo ati ndi okhonzeka kuthana ndi umphawi wamaphunziro omwe wafika pa 87 perecenti omwe ulipo makamaka msukulu za dziko lino zomwe zikubwezeretsa maphunziro pambuyo.

Izi zinanenedwa pamene bungwe lowona nkhani za maphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) linali ndi nkumano ndi aphunguwa komanso mabungwe mu mzinda wa
Lilongwe omwe amakambirana njira yamakono ya Ed-Tech.

Ed-Tech ndi njira yamakono yamaphunziro yomwe imakhudzana ndi ndondomeko yamaphunziro amakono ndi cholinga chopititsa maphunziro patsogolo.

Poyankhura ndi atolankhani, phungu wa ku mpoto kwa dera la Thyolo Ephraim Nayeja anati ndiwokhunzika komanso achisoni chifukwa cha mavuto omwe msukulu za dziko lino.

A Nayeja adawonjezera ponena kuti nkhani yokhudza zipangizo zogwiritsira ntchito pophunzitsa komanso kuchepa kwa aphunzitsi ndi zina zotsamwitsa zomwe ndi vuto lalikulu m’dziko lino.

“Ife ngati aphungu a nyumba yamalamulo tikayesetsa kuti pamene tikukumana mu mwezi wa novembawu tikakambirane zimenezi cholinga choti unduna wa zamaphunziro upatsidwe ndalama zokwanira zogwiritsira ntchito popititsa patsogolo maphunziro m’malawi muno. Tiyesetsa kuti tikumane ndi anduna a zachuma komanso ma bungwe ena omwe angatengepo pa mbali potithandidza kuti maphunziro ayende bwino,” a Nayeja adatero.

Poyankhulapo, Mkulu wa bodi ya Bungwe la CSEC Limbani Nsapato wati dziko lino likuyenel kupeza njira zosiyanasiyana zoti zithandizire kuti vuto la umphawi wamaphunziro lichepe pogwiritsa ntchito njira zamakono za tekinologe.

Iwo anatinso ana asuluku atha kumagwiritsa ntchito ngati ma foni amakono komanso ma kompyuta kuti athe kupeza mabuku ndipo zonsezo zingatheke ngati pangakhale ndalama zokwanira zogwiritsira ntchito pa maphunzirowa.

Advertisement