Kwacha yagwanso

Advertisement
Wilson Banda is the governor of the Reserve Bank of Malawi which is the central bank in Malawi

Ndalama ya Kwacha ikupitirira kutsika mphamvu pansi pa ulamulilo wa a Lazarus Chakwera.

Banki yaikulu ya Reserve Bank of Malawi (RBM) yalengezs kuti ndalamayi tsopano izigulidwa pa K1,180 pa Dola imodzi ya ku Amerika, kuchoka pa K1,126 pa Dola imodzi.

Malingana ndi mkulu wa Banki ya Reserve a Wilson Banda, kugwaku kwachitika potsatira malonda a ndalama zakunja omwe RBM inachita ndi makampani ovomerezeka ogulitsa ndi kugula ndalama zakunja.

Kugwa kwa Kwachaku ndi kwachinayi kuyambira mwezi wa Januwale chaka chino.

Odziwa za chuma akumati kugwa kwa Kwacha kukumapangitsa kuti anthu azigula katundu wochokera kunja pa mtengo okwera zomwe zimachititsa kuti mitengo ya katundu mdziko muno izikweranso.

Pakadali pano, anthu m’dziko muno ali kale pamoto poti mitengo ya zinthu zofunikira monga chimanga, mafuta, madzi ndi magetsi ndi yokwera kale.

Advertisement