Anthu ena apha mayi oyembekezera ndi mamuna wake ku Dedza

Advertisement

Anthu ena dzulo ku Magomero m’boma la Dedza apha mayi oyembekezera ndi mamuna wake ataotcha nyumba yomwe awiriwa amagonamo.

Phungu wa delari a Auzious Chidovu watsimikizira wailesi ya Zodiak za nkhaniyi.

A Chidovu ati munthu wina adabwereka ndalama kwa banjalo ndipo ndalamayo imamukanika kubweza.

Pofuna ndalama zake, bambo amene wamwalirayu anakalanda matumba atatu a chimanga kwa okanika kubweza ndalama uja.

Anthu ena akuti anakwiya ndi kulandidwa kwa chimangacho ndipo anakatentha nyumba yomwe mayi oyembekezera ndi mamuna wakeyo amagonamo.

Awiriwa afera mnyumbamo ndipo maliro akuyembekezeka kuikidwa lero.

Apolisi sanalankhulepo kanthu pa zankhaniyi.

Advertisement