Fetereza sitigula ngati chitumbuwa – Chihana wauza boma la Tonse

Advertisement

…wati ngati atsogoleri sakudziwa kanthu za feteleza, afuse anzawo omwe akudziwa

Mtsogoleri wa chipani cha Alliance For Democracy (AFORD) a Enock Chihana, wawuza akuluakulu a boma la Tonse kuti ngati sakudziwa zoyenera kuchita pa nkhani yogula fetereza, afuse zipani zina zomwe zili ndi ukadaulo ponena kuti fetereza samagulidwa ngati zitumbuwa.

A Chihana amayankhula izi lachiwiri pa 4 July, 2023 pa bwalo la masewero la Bvumbwe Research m’boma la Thyolo komwe chipani chawo chinachititsa nsonkhano wokondwelera kuti chatha zaka makumi atatu (30) chikhazikitsidwile m’dziko muno.

Poyankhula kuchinamtindi cha anthu omwe anasonkhana pa malowa, a Chihana anasonyeza kusakondwa ndi mmene boma la Tonse motsogozedwa ndi a Chakwera likuyendetsera ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya AIP.

Iwo ati ngati sipakhala kusintha pakayendetsedwe ka ndondomeko iyi, aMalawi ayembeke njala ya dzaoneni kaamba koti dziko lino limadalira ulimi omwe umadalira fetereza kuti mbewu zichite bwino.

Apa mkuluyu anati vuto loyambilira lofunika kukonza pa nkhani ya fetereza ndi kapezekedwe ka ndalama zakunja mdziko muno ndipo atsindika kuti ngati ndalama za kunja zingapitilire kusowa mdziko muno, naye fetereza sapezeka.

“Ine ndikufuna ndilangize boma kuti nkhani ya feteleza ayitenge mwa siliyasi kuposa m’mene ayitengera nthawi yonseyi. Vuto lilipo ndiloti sikuti anthu mukalowa m’boma mumadziwa china chili chose, iyayi. Ndikwabwino kufusa azinzanu amene nkhaniyo akuidziwa bwino bwino akuthandizeni.

“Feteleza amachokera kutali ndipo mafakitale opanda feteleza ndiochepa. Fetereza timagulira ndalama zakunja. Nde ngati dziko lilibe ndalama zakunja, feteleza iwalani, komaso ngati mwaiwala feteleza, landilani njala yoti iphe anthu mdziko muno,” anatelo a Chihana.

A Chihana ati vuto lina lomwe aliwona pa nkhani ya feteleza m’dziko muno ndi nkhani yokozekera ponena kuti boma likumachedwa kuyamba ntchito yogula fetelezayu zomwe ati ndi vuto lalikulu kaamba koti feteleza amatenga masiku ochuluka kuti afike kuno ku mudzi.

“Chomwe ndikufuna ndipemphe kwa anzathu amene akuyendetsa boma mchakuti, feteleza sitigula ngati chitumbuwa kuti ndikapita pa msika nkachipeza ngati sindigula lero mawa nkachipezabe aphikaso. Feteleza timachita kupeleka oda (order). Muzipanga pulani nthawi ya bwino chifukwa feteleza kuti adzafike kuno amatenga masiku pakati pa 21 ndi 45,” anaonjezera a Chihana.

Mtsogoleri wa AFORD yu anapitilira kufotokoza kuti chipani chawo chikadzalowa m’boma, pologalamu ya AIP adzayisintha kuti idzakhale yokomera anthu onse mdziko muno.

Apa anati akadzatenga boma pologalamuyi adzayigawa pawiri; gawo loyamba lidzakhala la anthu ovutika omwe adzidzalembedwa maina ndi unduna owona za chitukuko, chisamaliro cha anthu ndi ulumali ndipo gawo lina lidzapelekedwa kuunduna wa za malimidwe ndipo opindura adzakhala alimi ang’onoang’ono komaso akuluakulu.

Chipani cha AFORD ndi chimodzi mwa zipani zingapo zomwe zakangalika kuchititsa misonkhano m’madera osiyanasiyana pomwe masiku akuthera ku chitseko kuti dziko lino lichititse chisankho mchaka cha 2025.

Advertisement