Zikukhala ngati oyimba m’dziko muno apeza golide ku America pomwe naye Patience Namadingo watengeka mtima ndi ulendo wa Lulu, ndipo naye wati akupita kukaimba ku South Bend, ku ‘mang’ina’ kuja.
Posachedwapa, oyimba angapo kuphatikizapo Lawrence ‘Lulu’ Khwisa, Limbani ‘Tay Grin’ Kalirani ndi ena, anapita m’dziko la mkaka ndi uchili komwe onsewa anaimba malo angapo.
Kupita kwa Lulu komaso Tay Grin ku America kunabweretsa nansanganya wa nkhani zomwe oyimba wa kale wa chamba cha hip hop Jolly Bro (JB) wakhala akusokolotsa kudzera pa tsamba lake la nchezo.
Malingana ndi JB, malo amene Tay Grin komaso Lulu anakayimba ku South Bend m’dzikolo, ndi pa ma tharaveni pomwe anati ndiposasililika ndipo anayelekeza ndi ku Bwandilo mumzinda wa Lilongwe.
Iye anati ku South Bend kumakhala ma tchona a m’dziko muno omwe wati ambiri mwa iwo akukhalira kudya mang’ina ndi nsima kumeneko.
“Ku South Bend anthu ake ndi a chimidzi. Ndi anthu osadziwa ndalama. Amangokuwalirani ku Malawi ngati ali ndi ndalama koma kuno ndi a mphawi angokhalira ngongole,” anatero JB.
Koma ngakhale JB anayankhula zonsezi, Namadingo wamanga malamba ndipo ulendo wake wapsa okayimba ku South Bend ndi malo ena m’dziko la United States of America.
Kudzera patsamba lake la fesibuku, oyimbayu yemwe wakwanitsa zaka 33 pa 28 May chaka chino, wati mayambidwe ake m’dziko la America akayambira ku Indianapolis pa 1 July chaka chino.
Iye wati kenako kukakhala mkokemkoke pomwe madansi akatsikire ku South Bend pa 8 July, kenaka ku New York, Seattle, Oregon ndi Atlanta.
“Aka ndikachiwiri kuti Doc akaimbe m’dziko la America. Koyamba ndinakaimba ku Washington, Chicago ndi South Bend mu 2018. Ulendo uno ndikayambira kuyimba ku mzinda wa Indianapolis ku Indiana loweruka pa 1 July. Pezani ma tikiti anu pomwe Doc akubwera kachiwiri ku America,” walemba choncho Namadingo pa tsamba lake la fesibuku.
Nkhaniyi yabweretsa chimwemwe chodzadza tsaya kwa JB yemwe m’mbuyomu anabwera poyera ndikuwulura kuti iye amasangalatsidwa ndi ukatswiri wa Namadingo.
JB walemba patsamba lake la fesibuku kuti kupita kwa Namadingo ku America, “Kuzakhala chi dansi cha mwana ali pati.”
Follow us on Twitter: