Nyimbo udayimba ndi Mafo ilikuti? Amalawi afunsa Gwamba

Advertisement

Amalawi adabwa ndikuchedwa kutuluka kwa Nyimbo yomwe Katswiri wachamba cha hip hop Gwamba adaimba ndi Madala Mafo mu chaka cha 2020.

Gwamba adalonjeza mtundu wa Amalawi kuti ausa Mafo kwa akufa muchakachi. Ndipo adatsimikiza izi pa ma tsamba ake amchezo. Ngakhale adatero, pano talowa chaka chachiwiri Nyimbo yi isadatuluke.

Ndipo izi zapangisa a Malawi kufusa katswiriyu kuti zili pati? Anthu adabwanazo chifukwa oimbayu wakhala akutulusa nyimbo zambiri mkuiwaala yakalekale yi.

Othilira ndemanga pauthenga wake wapompano omwe Gwamba walengeza kuti atulusa nyimbo yasopano pa 7 Febuluwale ndi myamata otchedwa Quest, alangiza oimbayu kuti atuluse Kaye nyimbo yomwe adaimba ndi Mafo.

Mukulankhula kwawo a Andrew Mbulukwa amene ali mmodzi mwa omusata Gwamba adati, “Mudakayambira kutulutsa Nyimbo mudaimba ndi Mafo ijatu.”

Nawonso a Bright Noah pothilira ndemanga pa uthengau anena kuti Khumbo la Amalawi ndiloti atuluse nyimbo yomwe adaimba ndi Madala Mafo.

Gwamba amene dzina lake lakubadwa lili Duncan Zgambo adanenetsa kuti salora kuti luso la Mafo life, patapita nthawi yaitali mnyamatayu asadatuluse nyimbo. Ndipo izi zidabweresa chiyembekezo chokhathamira pakati pa Amalawi potengera kuti Mafo wasowa kwanthawi yaitali.

Mafo adatchuka zaka khumi zapitazo ataimba nyimbo zingapo ndi nzake otchedwa Shozi. Dzina mwa nyimbozi ndi akazi amapha komanso mowa.

Madala Mafo amakondedwa ndi Amalawi ambiri ngakhale watenga nthawi osaphika nyimbo. Omukonda amanena kuti ndi mmodzi mwa oimba odekha komanso opanda mantha akalowa mu studio.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.