Amuna awiri amangidwa chifukwa chokupha munthu ku Mzimba

Advertisement
Zosiyilana Hara - Dan Mphande

Apolisi ya Jenda ku Mzimba, amanga Zosiyilana Hara wazaka 34, ndi Dan Mphande wazaka 29, powaganizira kuti adapha a Komani Nyoni omwe adapezeka atamwalira pa 28 July 2024 ku Champhira m’bomali. 

M’neneri wa polisi ya Jenda Macfarlen Mseteka wati awiriwa adamangidwa usiku wa pa 7 August 2024 a polisi atachita kafukufuku.

Malinga ndi zomwe apolisi anapeza, malemu Nyoni adachoka kunyumba kukamwa mowa ku Zosiyilana Pub pa 27 July 2024 ndipo sanabwererenso kwawo zomwe zinachititsa makolo ake kuti ayambe kuwafufuza koma sanawapeze.

Thupi la malemuwa linapezeka pa tchire la champhira.

Malinga ndi ripoti la ku chipatala, Nyoni anafa kamba ka ululu wazilonda zomwe zinali zokhapidwa.

Awiriwa akuimbidwa mlandu wakupha malingana ndi gawo 209 la malamulo oyendetsera dziko lino. 

Hara and Mphande onse amachokera mmudzi mwa mfumu yayikulu Mabilabo m’boma la Mzimba.

Advertisement