Silver Strikers yatosa pa Bala la Wanderers kuthetsa maloto ake a Top8

Advertisement
Bingu stadium

Ukali wa Silver Strikers chaka chino wawonekanso usiku wa loweluka pa masewelo a mu ndime ya ma Timu anayi ya mu Airtel Top8 pa bwalo la Bingu mu nzinda wa Lilongwe pamene yaswa mtima wa Mighty Mukuru Wanderers omwe ndi osweka kalenso.

Atayambitsa masewelo Easter Zimba, anyamata a ku Lilongwe anawona kuti nthawi sili ku mbali yawo ndipo anachitilatu dongosolo lophwanya anyamata a ku Lali lubani pa mphindi ya chi 8 kudzera mwa Binwell Katinji kutsatira mphungwepungwe omwe otchinga kumbuyo a wanderers anachita.

Mpira omwe unali otentha ndi othamanga mphindi zonse, chigawo choyamba chinatha ma Banker akutsogola 1-0.

Ma bomba ndi ukali zinavumba ku ma golo onse awiri la Richard Chipuwa komanso wakale wa Chitipa United George Chikooka koma awiriwa anawonetsetsa kuti ukaliwu usadzetse chisangalalo pa anzawo pamene anakaniza golo kangapo konse.

Oyimbira Easter Zimba anapeleka chikalata chotulukira kwa Nickson Mwase pa mphindi ya chi 76 chifukwa cha kusasewera bwino pamene Nickson Mwase anavulaza Thierry Tanjong Sama ndipo wanderers inagwiritsa ntchito kupelewera kwa Silver kuti ipeze mwayi koma sizinaphule kanthu.

Mphindi za ku mapeto Mighty Mukuru Wanderers inapsa mtima ndipo inali alendo obwerabwera pa golo la Chikooka koma tsiku la tsoka umatentha ndi wa dzana zonse sizinaphule chigoli chofananiza kuti mwina ma penate akaweluze ndipo masewelo anatherabe 0-1 kukomela a ma Banker.

Mphunzitsi wa Silver Strikers Peter Mponda wati masewelo a loweluka ndi Wanderers anali ovuta kwambiri koma osangalatsa ndipo ati akuyembekeza ndi chidwi kukachita bwino mu masewelo otsiliza ndi timu yomwe ingachite bwino mu semi fayinolo ya chiwiri.

Iye anati mchigawo chachiwiri chonse anali pa phuma kwambiri chifukwa cha m’mene adani awo amasewelera.

Meke Mwase yemwe ndi Mphunzitsi wa Wanderers anati anyamata ake akumagoletsetsa zigoli mwa msanga masiku ano zomwe wati zimakhala vuto kwambiri m’masewelo ndipo wati zatelemu maso ali ku league.

Pamapeto pa masewelo a loweluka Binwell Katinji ndiye anasankhidwa kuti ndi dolo wa masewelo a pakati pa Silver ndi Wanderers.

Silver strikers ikuyembekezera kudzaswana ndi opambana m’masewelo a Lamulungu pakati pa FCB Nyasa Big Bullets ndi Kamuzu Barracks.

Advertisement