Abale sakudziwabe komwe kuli Chiyanjano Mbeza

Advertisement
Chiyanjano Mbeza

Patadutsa maola oposa 24 apolisi chimangileni mkozi wa nyimbo, Chiyanjano Mbeza pa mlandu omwe sukudziwika, achibale ake ati mpaka pano sakudziwabe polisi yomwe m’bale wawoyu akusungidwa.

Mbeza yemwe amajambula nyimbo munzinda wa Blantyre, anamangidwa madzulo a Lolemba sabata ino pa zifukwa zomwe mpaka pano sizikudziwika.

Ganizani Mbeza yemwe ndi mchimwene wake wa Chiyanjano, Lachiwiri anauza nyumba zina zosindika nkhani m’dziko muno kuti m’bale wawuyo atamangidwa ku HHI munzinda wa Blantyre anakwezedwa galimoto ndipo anauzidwa kuti akumutengera ku polisi ya Lilongwe.

Ganizani wati pomwe achibale ena amalondora galimoto yomwe idatenga Chiyanjano, ali mkati mwanjira galimotoyo idawasowa ndipo atafika ku Lilongwe komwe adauzidwa kuti akumutengera Chiyanjano adadzidzimuka m’mawa wa Lachiwiri kumva kuti m’bale wawo watengeredwa ku Mangochi osati Lilongwe.

Iwo ati ngakhale anauzidwa za ku Mangochi, “Pakadali pano, Chiyanjano salinso ku Mangochi chifukwa abale omwe adapitako sanamupeze ndipo tikupempha apolisi kuti atiwauze komwe kuli m’bale wathu kuti tizitha kukamuona.”

Iwo apempha apolisi kuti awafotokozere komwe kuli Chiyanjano komaso zifukwa zomwe apolisi amumangira m’bale wawoyu.

Dzulo Lachiwiri, wachiwiri kwa mneneri wa polisi a Harry Namwanza anawuza nyumba zina zofalitsa nkhani kuti iwo akulondoloza nkhaniyi ndipo ayankhula zambiri akupeza mauthenga okwanira pa nkhaniyi.

Ngakhale sizikudziwika kuti Chiyanjano wamangidwira chiyani, mphekesera zikuveka kuti mkozi wa nyimboyu akumuganizira kuti amajambula ndikutulutsa mauthenga onyoza boma omwe amatulutsidwa ndi Bakili Muluzi TV.

Advertisement