Mumangidwa! Khonsolo ya Lilongwe yaletsa kufukula mchenga

Advertisement
Lilongwe City Council

Ngati mumafuna kupeza kakhobidi kudzera m’magobo ofukula m’chenga komaso miyala mkati mwa nzinda wa Lilongwe, pezani zina zochita kamba koti khonsolo ya nzindawu yati ikuthirani dzingwe.

Khonsolo ya mnzinda wa Lilongwe yatulutsa kalata yomwe wasayinira ndi nkulu wa khonsoloyi Macloud Kadam’manja yochenjeza mchitidwe ofukula mchenga komaso miyala mkati mwa mnzindawu popanda chilolezo.

Mu kalatayi, khonsoloyi yati, “anthu okhala munzindawu komanso ofukula m’chenga popanda chilolezo aleke kutenga minda ya khonsolo, kukumba mchenga ndi miyala popanda chilolezo cha khonsoloyi.

“Munthu aliyense kapena magalimoto omwe angapezeke akufukula ndikukweza mchenga mosaloledwa mkati mwa mzindawu, adzakhala olakwa ndipo adzapeleka chindapusa kapena kumangidwa malinga ndi malamulo akhonsolo pa za chilengedwe.”

Khonsoloyi yadziwitsaso anthu onse kuti kuyambira pa 9 July, 2024, iyamba kumanga anthu ofukula m’chenga popanda chilolezo ndi kulanda milu ya mchenga yomwe idzapezeke paliponse mkati mwa mzindawu popanda chilolezo cha khonsolo.

Mali ng anta ndi kalatayi, khonsoloyi ikutsindika ndikukumbutsa anthu okhala munzondawu kuti aliyense amene adzapezeke akuphwanya malamulowa adzakumanizana ndi lamulo.

Advertisement