Ophunzira pa Mzuni alanga wakuba

Advertisement

M’nyamata wina amene wakhala akunamizira kuti ndi ophunzira pasukulu ya Ukachenjede ya Mzuzu ali mu uluru osaneneka kutsatira kumenyedwa ndi ophunzira pasukukuyi pomuganizira kuti anaba mafoni awiri awophunzira ena.

Amon Chimalawalana, yemwe watiuza nkhaniyi, wati lero pasukuluyi panali masewero ndipo ophunzira omwe anali kusewera mpira anasunga mafoni awo pa malo ena ndipo atatuluka anapeza kuti mafoniwo asowapo.

Mnyamatayu wamenyedwa molapitsa.

Mkulu wina anati anamuona m’nyamatayo akupakulapo mafoniwo chapatali koma panthawi imeneyi mkuti wakubayo anali atasowapo kale.

Apa anampeza wakubayo ndikumufunsa ngati ali ophunzira wapasukulupo, koma zimaonetsa kuti wakubayo saphunzira pasukulupo. Apa kunali kumenya wakubayo mpaka kufika pomusintha maonekedwe.

Pakadali pano zikumveka kuti wakubayo anatengeledwa kuchipatala kutsatira kumenyedwa kwambiri ndi ophunzirawo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.