Abambo ambiri sanayezetse magazi, atsikana achichepere akutenga HIV kwambiri – yatelo NAC

Advertisement

Bungwe lotsogolera ntchito yolimbana ndi matenda a Edzi la National Aids Commission (NAC), lati kafukufuku akuonetsa kuti a bambo ambiri akumangodziyendera osayezetsa magazi pomwe akuti atsikana a chichepere makamaka m’sukulu zaukachenjede ndi omwe akutenga kwambiri kachiromboka kamba ka “ma blesser”.

Izi ndi malingana ndi mkulu owona zopewa kachirombo ka HIV ku bungwe la NAC a Francis Mabedi omwe amayankhula izi Lachinayi pomwe bungweli limaphunzitsa atalonkhani pansi pa bungwe la Blantyre Press Club za lamulo lokhudza matenda a Edzi.

A Mabedi ati mwa a bambo 100 aliwose, a bambo 41 amangodziyendera osadziwa ngati ali ndi kachirombo ka HIV kapena ayi, chomwe ndi chiwerengero chokwera kuyelekeza ndi chiwerengero cha amayi chomwe chili pa amayi 15 mwa 100 aliwose.

Mbali inayi, chiwerengero cha ana omwe samadziwa ngati ali ndi kachirombo ka HIV kapena ayi chili pa ana 23 mwa 100 aliwose ndipo zadziwika kuti amayi oyendayenda ndi ena mwa magulu omwe amakonda kuyezetsa kamba koti mwa amayi oyendayenda 100, m’modzi yekha ndi yemwe sanayezetsepo magazi.

A Mabedi ati chiwerengero cha abambo osayezetsa ndichokwera kwambiri kamba koti a bambo ambiri amazemba kupita ku chipatala komaso ambiri amatanganidwa ndi ntchito zomwe amagwira.

“Abambo ambiri omwe ali ndi HIV koma sanayezetse chiwerengero chawo nchachikulu kuyerekeza ndi cha amayi. Pafupifupi 41% ya abambo sakudziwa kuti mthupi mwawo muli bwanji.

“Izi zili chonchi chifukwa a bambo ambiri amakhala ali ku ntchito, mwina kutanganidwa zomwe zimapangitsa kuti mauthenga okhudza nkhani za HIV aziwamva mwa apo ndi apo kusiyana ndi amayi,” atelo a Mabedi.

Iwo ati pano bungwe la NAC layika njira zosiyanasiyana zofuna kuwonetsetsa kuti mauthenga okhudza matenda a Edzi, adzifikira a bambo ochuluka ndicholinga choti a bambo ambiri adzipita ku chipatala kukayezetsa HIV.

Pa nkumanowu, a Mabedi anatiso kafukufuku akuwonetsa kuti atsikana a zaka za pakati pa 15 ndi 24 ndi omwe akutenga kwambiri kachirombo ka HIV.

Apa anati mwa anthu 100 atsopano omwe akutenga HIV, 22 akumakhala atsikanawa ndipo akuti ambiri mwa iwo ndi atsikana am’sukulu za ukachenjede omweso anati akumachita zibwezi zogonana ndi azibambo pofuna thandizo.

“Mwa anthu atsopano omwe akutenga ka chirombo ka HIV, atsikana achichepere akuchulukirapo pafupifupi 22%. Izi ndi kamba koti ambiri mwa iwo amakhala akusaka ndalama ndi ma thandizo ena.

“Tili ndi achitsikana ambiri amene akudzikhalira okha m’masukukulu nde zofuna zawo kuti azipeze amatha kupezeka kuti azibambo ena awanyengelera kuti agone nawo mosadziteteza mkumapezeka kuti akutenga HIV,” anaonjezera choncho Mabedi.

Mkuluyu wati m’mizinda ya Lilongwe, Blantyre, Mzuzu, ndi Zomba ndiyomwe ili ndi chiwerengero chokwera cha anthu atsopano omwe akutenga ka chirombo ka HIV ndipo akuti izi ndi kamba koti m’mizindayi muli ophunzira ambiri a m’sukulu za ukachenjede.

Advertisement