Kupha nsomba mosatsata malamulo kukuchulukira mnyanja ya Chirwa

Advertisement

Mchitidwe okupha nsomba mosatsata malamulo ukuchulukira mnyanja ya Chilwa chifukwa cha kuchuluka kwa chiwerengero cha anthu amene amakhala mozungulira nyanjayi.

Mkulu oyang’anira kaphedwe ka msomba m’boma la Zomba, Elliot Lungu wati kuchuluka kwa anthu kukukolezera mchitidwe okupha msomba mwachisawawa.

Mau ake, Lungu wapempha mabungwe ndi anthu okhala mozungulira nyanja ya Chilwa kuti atenge gawo kuteteza nsomba mu nyanjayi .

Kuyambila chaka cha 2012 nyanjayi yakhala ikupindulitsa anthu oposera 1.5 miliyoni kudzera mu ulimi wa thirira komaso kupha nsomba mma boma a Zomba, Machinga komaso Phalombe.

Koma chifukwa cha kuchepa kwa madzi, mayendedwe a pa thunda komaso kusowa upangiri kwa adindo ndi zimene zimabwezeretsa mbuyo tchito yoteteza nyanjayi.

Advertisement