Tinali akapolo, ndagwililidwa ndi amuna angapo – amayi aulura nkhaza za ku Oman

Advertisement

Amayi omwe adali mdziko la Oman komwe anapita atanamizidwa kuti adzikapatsidwa malipilo ochuluka, achenjeza atsikana ena kuti asamakhumbileko ponena kuti ku dzikoli kuli ukapolo osasimbika, ndipo wina waulura kuti wakhala akugwililidwa ndi bwana komaso anzake a bwana wake.

Zaka zingapo zapitazo makamaka kuyambira chaka cha 2021, m’masamba a nchezo mwakhala mukuyenda nkhani ya asungwana omwe anatengedwa m’dziko muno kupita dziko la Oman ponamizidwa kuti kumeneko kuli nsipu obiliwira.

Zadziwika tsopano kuti nsipu obiliwira umanenedwawo unali othilidwa tameki kamba koti azimayi angapo omwe anaonjoka m’sampha umenewu, afotokoza tsatane tsatane wa mazuzo omwe akhala akukumana nawo pomwe anali kusaka chilembwe mdziko la Oman lomwe ndi limodzi la mayiko a aluya.

Izi zadziwika potsatira nkhani yomwe BBC’s Africa Eye yatulutsa yokhudza nkhaza zomwe amayi ochuluka ochokera m’dziko muno akhala akukumana nazo akafika m’dziko la Oman koma ambiri mwa iwo amapita nchimbulimbuli kamba konamiza ndi anthu ena omwe amadzitchula kuti opezera anzawo ntchito.

BBC Africa Eye yakamba za amayi angapo kuphatikizapo nzimayi wina yemwe yamutcha Georgina yemwe akuti anakumana ndi mazanga zime m’dziko la Oman komwe anapita kukagwira ntchito ya m’nyumba, mpaka akuti anayamba kulingalira zodzikhweza kamba kosweka mtima komaso kusowa chiyembekezo.

Mwazina, Georgina wauza BBC kuti wakhala akugwiliridwa ndi a bwana ake omweso akuti akatelo amakatenga anzawo ena angapo kudzagonana nayeso ndipo pamapeto pake iwowo amalandira ndalama za nkhani nkhani kuchokera kwa azinzawowo ngati malipiro.

Nkhani ya Georgina yemwe ndi wa zaka 32, inafika povetsa chisoni pomwe iye anayamba kulira pa nthawi yomwe amafotokoza zakuti bwana akewo kenaka anayamba kumamugona pa chiwalo chake chochitira chimbudzi ndipo wati anali ndi mabala.

Kupatula Georgina, mayi winaso yemwe anacheza ndi BBC ndi Blessings wa zaka 39 yemwe ndi m’modzi wa amayi 54 omwe anabwelera kuno kumudzi chaka chatha mothandizidwa ndi boma la Malawi lomwe akuti linagwiritsa ntchito ndalama zosachepera K200 miliyoni.

Blessings naye anaulura kuti nayeso ankachitilidwa nkhaza ndi a bwana ake m’dziko la Oman ndipo akuti nthawi ina anapsa ndi madzi otentha pomwe ankaphika koma wati ngakhale anali ndi mabala owopsa, bwana akewo ankamukakamiza kumagwirabe ntchito.

Kudzera mu nkhaniyi, zadziwika kuti a Malawi ambiri mdzikoli samaloledwa kupuma pa ntchito ndipo akadwala samathandizidwa ndi ma bwana awo, ndipo umboni wake unaoneka pa nkhani ya Ida Chiwalo wa ku Mangochi yemwe anamwalira m’dzikoli kamba kosathandizidwa nsanga pomwe iye amadwala.

A mayi 54 omwe anabwelera mdziko muno ku chokera ku Oman, anathandizidwa ndi Pililani Mombe Nyoni yemwe analumikiza ndi Ekaterina Porras Sivolobova yemwe ndi mkulu wa bungwe lothandiza anthu ozembetsedwa la ‘Do Bold’ lomwe likulu lkae lili mdziko la Greece.

Porras Sivolobova ndi yemwe analumikizana ndi akuluakulu a boma la Malawi lomwe linapulumutsa amayiwa chaka chatha koma zikuveka kuti a Malawi ena anakali mdziko la Oman komwe akusowekerabe thandizo kuti abwelere kuno ku mudzi.

Zadziwikaso kuti anthuwa akufuna kubwelela kumudzi kuno amakanizidwa ndi ma bwana awo ndipo amauzidwa kuti ngati akufuna kubwelera kuno, abweze kaye ndalama za nkhani nkhani zomwe ma bwanawo anapeleka kwa anthu opezera anzawo ntchitowo.

Izi zikutanthauza kuti anthuwa akamapita mdziko la Oman amakhala kuti agulitsidwa ndi anthu opezera anzawo ntchitowo ngakhale kuti eni akewo samadziwa zoti anagulitsidwazo.

Advertisement