Nzika zauza Escom kuti ikonze magetsi pasanathe maola 24

Advertisement
People in Balaka protesting at ESCOM offices in the district

Gulu la nzika zokhudzidwa ndi vuto la magetsi ku dera la Majiga 2 m’boma la Balaka lapeleka maola 24 ku kampani ya Escom kuti likonze vuto la magetsi lomwe akukumana nalo.

Gululi kum’mawaku lidachita ziwonetsero pofuna kumema kampani yogawa komanso kugulitsa magetsiyi kuchita machawi pothana ndi vutoli.

Anthu m’delari tsopano akhala opanda magetsi kuyambira pa 22 February chaka chino chifukwa makina a transformer amene akuti adapsa.

Malingana ndi oyimila gululi, a Pretorius Halidi atiuza kuti vutoli lasokoneza ntchito za malonda, kulimbikitsa mchitidwe wa umbava komanso umbanda kuphatikizanso kusokoneza maphunziro a ana awo omwe akuti pakadalipano ali kalikiliki kukonzekera kulemba mayeso a sitandade 8, fomu 2 komanso fomu 4.

Anthuwa ati amema  nantindi wa anthu ena kuchita ziwonetsero za mtima bii ngati Khumbo lawo silikwanilitsidwa pakutha pa maola omwe apelekawa.

Ndipo m’mawu ake, m’modzi wa akuluakulu a kampani ya Escom yemwe wapempha kuti tisamutchule dzina lake wati apeleka madandaulowa koyenelera.

Advertisement