MEC ipeleka zipangizo za BVRKs ku bungwe la NRB

Advertisement
MEC

Ngati njira imodzi yowonetsetsetsa kuti anthu ambiri mdziko muno ali ndi chiphaso cha unzika chomwe chingawathandizile kulembetsa mu kaundula wa voti, bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) liri ndi malingaliro opeleka zipangizo za Biometric Voter Registration Kits (BVRKs) ku bungwe lowona za kalembera la National Registration Bureau (NRB).

Malingana ndi chikalata chomwe wasainila ndi mkulu oyendetsa zisankho ku bungwe la MEC, Andrew Mpesi, chati bungwe la NRB lidawapempha kuti alipatse makina a BVRKs okwana 261 kuti liwathandizire mu ntchito ya kalembera wa nzika yomwe ili mkati pakadali pano.

“Bungwe la NRB likufunitsitsa kufikira anthu m’madera ambiri mdziko muno mu kanthawi kochepa zomwe zithandizile bungwe la MEC pa kalembera wa anthu oyenera kuponya vuto mu zisankho zomwe zikubwera chaka cha mawa,” adafotokoza a Mpesi.

Bungwe la MEC silidzagwilitsa ntchito makina a BVRK mu kalembera wa anthu oyenera kuponya voti pa chisankho cha chaka chamawa ndipo likuyembekezeka kuzagwilitsa ntchito makina omwe lidagula posachedwapa a Elections Management Device (EMD).

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.