Wagamulidwa kukakhala kundende zaka 63

Advertisement

Bwalo la milandu ku Lilongwe lalamula a Arafat Goman kukakhala kundende kwa zaka 63 pa mlandu wakupha a Cecilia Lucy Kadzamira azaka 82 amene adali mchemwali wa a Tamandani Kadzamira, mthandizi wa mtsogoleri wakale wadziko lino a Dr Hastings Kamuzu Banda.

Mkuluyu adazengedwa mlanduwu mchaka cha 2019 ndipo oweruza milandu a Zondi Mvula wati wapereka chilango chokhwimachi kwa mkuluyu pofuna kupereka phunziro kwa anthu kuti aziremekeza anthu okalamba.

A Zondi Mvula anapitilizanso kufotokoza kuti mkuluyu adapha gogoyu mwankhaza.

Kadzamira adapezeka atafa m’nyumba mwawo ku Area 47 ku Lilongwe. Ndipo apolisi atachita Kafukufuku adapeza womaliza kuyankhulana ndi gogoyu adali a Gomani. Apa apolisi adakwanitsa kumunjata mkuluyu.

Advertisement