Mutharika ayankhula ndi a Malawi Lachisanu lino

Advertisement
DPP president Peter Mutharika

Lachisanu lino chidwi cha anthu chikhala ku Mangochi ku nyumba ya Page komwe mtsogoleli wa chipani cha Democratic Progressive (DPP), Professor Peter Mutharika, akhale akuyankhula ku mtundu wa a Malawi kudzera pa msonkhano wa atolankhani omwe achititse.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe chipani cha DPP chatulutsa momwe akudziwitsa anthu kuti a Mutharika achititsa nsonkhano wa olemba nkhani ku nyumba yawo ya Page m’boma la Mangochi Lachisanu lino pa 8 March, 2024.

Izi zikubwera pomwe mtsogoleri wa dziko lino opumayu masiku apitawo anayimitsa kaye nsonkhano wa atolankhani ngati omwewu, ndipo m’malo mwake chipani cha DPP chinati nsonkhanowo uchitikabe ku tsogolo kuno.

Malingana ndi akuluakulu a chipani chotsutsa bomachi, a Mutharika ali ndi uthenga omwe akufuna awuze a Malawi komanso akuti pali uthenga wina opita kwa mtsogoleli wa dziko lino a Lazarus Chakwera.

Zonsezi zinayamba ndi mtopola omwe anthu ena omwe akuganizilidwa kuti ndi a chipani cha Malawi Congress (MCP) anachitira mamembala a chipani cha DPP pomwe amafuna kuchititsa misonkhano yoyimayima munzinda wa Lilongwe masiku apitawa.

Anthu amtopolawa anaphwanya galimoto zingapo za chipani cha DPP pomwe enaso anamenya ndikuvulaza mamembala ena a chipani chotsutsachi zomwe zinapangitsa akuluakulu a chipani cha DPP kulengeza kuti a Mutharika akhala akuyankhula ku mtundu wa aMalawi sabata yatha.

Pakadali pano, anthu ali ndichiyembekezo kuti mwa zina a Mutharika akhala akudzudzula mchitidwe wa chipolowe omwe unachitikawu komaso kudzudzula zinthu zina zomwe chipanichi chakhala chikudandaula kuti sizikuyenda bwino.

Advertisement