Tithandiza anthu amene ali ndi vuto la njala, yatero banki ya NBS

Advertisement

Banki ya NBS yalonjeza kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi njala dziko muno.

Mkulu wa nthambi ya bankiyi ku Limbe, Twaibu M’nani, anayankhula izi dzulo pa 18 February, 2024, m’boma ya Chiradzulu kumene bankiyi imagawa ufa wa chimanga wa ndalama zokwana 3.5 miliyoni ku maanja 150 amene akhudzidwa ndi vuto la njala.

Mu mau ake, mfumu yaikulu Phunga yayamikira bankiyi chifukwa cha thandizo lomwe lafika mu nthawi yake ndipo anapitiriza kunena kuti dera lake anthu akhudzidwa kwambiri ndi vuto la la njala ndipo akumadalira mzimbe ngati chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku.

Nthambi yoona kusintha kwa nyengo dziko muno ikupitiriza kulosera ng’amba yomwe ikhudze kwambiri m’madera ambiri a chigawo chakum’mwera.

Advertisement