Mutale watutumutsa gulu ndi uthenga okhudza bwenzi lake Tay Grin

Advertisement
Mutale Mwanza Zambian socialite in Malawi

Ubwenzi wa Tay Grin ndi Mutale Mwanza ukuoneka uli pendapenda potsatira uthenga omwe mkaziyu walemba pa tsamba lake la mchezo.

Uthengawu ukusonyeza kuti mkaziyu wasweka mtima ndi zomwe bwenzi lake la muchita ngakhale zifukwa zake sanapereke ndipo  ukusonyeza kuti ubale wa awiriwa sukuyenda bwino.

“Ngakhale titasiyana nthawi ya 11 koloko, dziwa kuti imakati 11:1 koloko ndipeza wachikondi wina,” mbali imodzi ya uthengawu.

Izi zili chomwechi pamene zikumveka kuti Tay Grin analephera kukaona bwenzi lake ku chipatala  pa 14 February, 2024 lomwe ndi tsiku la anthu amene ali mu chikondi.

Kumayambiliro kwa mwenzi wa February, Mutale Mwanza anadwala kwambiri ndipo anagonekedwa ku chipatala koma kafukufuku akusonyeza kuti Tay grin sanapite dziko la Zambia kukazonda bwenzi lakero.

Ubwenzi wa awiriwa unadziwika bwino kumapeto kwa chaka chatha ndipo awiriwa amayenderana pafupipafupi.

Pakali pano, anthu pa masamba a mchezo atutumuka ndi zomwe walemba Mutale ndipo akufunsa chomwe walaka Tay Grin pomwe ena akuti Mutale amukhululukire oyimbayu.

Advertisement