Wanjatidwa kaamba kogwililira mwana wake yemwe ndikumpatsa pathupi

Advertisement

Bambo wina wa zaka 32 zakubadwa akusungidwa mchitokosi cha apolisi ku Monkey-Bay m’boma la Mangochi kaamba komuganizira kuti wakhala akugwililira mwana wake wa zaka 12 mpaka kufika pomupatsa mimba.

Alice Sichali yemwe ndi mneneri pa polisi ya Monkey-Bay wati bamboyu dzina lake ndi Moffat Phiri akumusunga mchitokosi kamba koti akumuganizira kuti wakhala akuchita zadama ndi mwana wake mpaka kumupatsa mimba.

Malingana ndi mneneriyu, a Phiri akhala akutengerapo mwayi pa mwanayu kamba koti amayi ake ali ndi vuto losamva.

Phiri amachokera m’mudzi mwa Yusuf kwa mfumu yaikulu Nankumba m’boma lomweli la Mangochi ndipo posachedwapa akaonekera kubwalo lamilandu posachedwapa kukayankha mulandu ogwililira komanso kupereka pa thupi kwa mwana wake yemwe.

Advertisement