Bushiri wayamba kugawa chimanga cha ndalama zokwana 14 biliyoni


Prophet Shepherd Bushiri yemwe ndi mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG) walengeza kuti wayamba pologalamu yogawa chimanga kwa maanja oposa 1 miliyoni omwe akhudzidwa ndi njala mdziko muno.

Malingana ndi a Bushiri omwe amayankhula izi kunkhokwe yosungira chimangachi, chimangachi chilipo chokwana 17,000 Metric tons, ndipo ndichandalama zokwana 14 biliyoni Malawi kwacha.

Bushiri wapemphanso anthu kuti azitha kugawa kochepa komwe ali nako ndipo iye anati akadatha kugulitsa chimangachi koma iye wati ndikwabwino kumaganizira anthu ena.

Iye wati thandizoli lifikira madera omwe adakhudzidwa ndi ng’amba komanso Namondwe wa Freddy.

Pofuna kuti ntchitoyu iyende bwino, Bushiri wati mpofunika kuti pakhale mgwirizano wabwino pakati pa akuluakulu akuboma komanso anthu wamba.

Iye wapemphanso mabungwe komanso makampani kuti agwirane manja pothandiza maanja omwe akuvutika ndi njala.

Wolemba: Ben Bongololo

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.