Mzuni itsekulira pa 19 m’malo mwapa 12 February

Advertisement
Mzuzu University is located in Mzuzu in the Northern Region of Malawi

Sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu yalengeza kuti ophunzira omwe akupitiliza maphunzilo pasukuluyi adzayamba maphunzilo awo amchigawo choyamba lolemba pa 19 February 2024 m’malo mwa pa 12 February.

Kudzera mchikalata chomwe Malawi24 yaona, sukuluyi ikudziwitsa anthu onse kuphatikizapo makolo ndi omwe amayang’anira ophuzilawa kuti yayika pa 19 February ngati tsiku loyambira maphunzilo kuchoka pa 12 February.

Mwazina chikalatachi chati kalembela wa ophunzirawa udzachitika pa 19 ndi pa 20 February ndipo ophunzirawa adzayamba kulowa mkalasi pa 21 February 2024.

Izi zadza pamene ophunzirawa ali ku tchuthi komwe adapita mmwezi wa January pa 15 ndipo mphekesera imamveka kuti adzatsekulira pa 12 February mwezi uno.

Wolemb

Advertisement