Nankhumwa atha kudzikumbira dzenje lomwe sangathe kutulukamo akapanda kusamala, watero katswiri pa ndale

Advertisement
Kondwani Nankhumwa

M’modzi mwa akatswiri pandale mdziko muno wachenjeza a Kondwani Nankhumwa kuti akuyenera kupanga chiganizo mosamala pa zatsogolo lawo pandale ponena kuti akapanda kusamala atha kudzikumbira okha dzenje lomwe iwo sangathe kutulukamo.

Malingana ndi Katswiriyu, a Lyford Chadza, a Nankhumwa akamapanga chiganizo chawo pazokhudza tsogolo lawo pandale asapusitsike kwambili ndi anthu omwe akuwachemerela kamba koti anthu amatha kusinthidwa dzuwa lili msana.

Katswiriyu anafotokozanso kuti iye akukhulupilira kuti chiganizo chomwe a Nankhumwa akhale akupanga chikhala chowapindulira pa tsogolo lawo pa ndale.

Masiku apitawo, a Nankhumwa adalengeza kuti akhala akulankhula ku mtundu wa amalawi kuwadziwitsa zokhudza tsogolo lawo pa ndale kutsatira atachotsedwa mchipani cha DPP.

Pakadali pano pali mphekesera yoti a Nankhumwa ayambitsa chipani chawo ktuti adzayimile nawo pa zisankho zomwe zikudzazi.

Advertisement